Mawu Ofotokoza Chigawo cha 14
Akhristu oyambirira analalikira uthenga wabwino wa Ufumu m’madera ambiri padzikoli. Yesu ankawatsogolera kuti adziwe kokalalikira ndiponso anawathandiza kulalikira m’zilankhulo zina. Yehova anawathandizanso kuti akhale olimba mtima komanso anawapatsa mphamvu kuti azipirira akamazunzidwa.
Yesu anaonetsa mtumwi Yohane masomphenya a ulemerero wa Yehova. M’masomphenya ena anamuonetsa Ufumu wakumwamba ukugonjetsa Satana ndiponso kumuchititsa kuti asamasocheretsenso anthu. Yohane anaona Yesu akulamulira limodzi ndi anthu 144,000. Anaonanso dziko lonse lili Paradaiso komanso anthu onse akulambira Yehova mogwirizana.
M'CHIGAWO ICHI
MUTU 94
Ophunzira a Yesu Analandira Mzimu Woyera
Kodi mzimu woyera unawapatsa mphamvu yodabwitsa yotani?
MUTU 95
Sanasiye Kulalikira
Atsogoleri achipembedzo amene anapha Yesu ankayesetsa kuletsa ophunzira ake kuti asamalalikire. Koma ophunzirawo sanasiye kulalikira.
MUTU 97
Koneliyo Analandira Mzimu Woyera
N’chifukwa chiyani Mulungu anatumiza Petulo kunyumba ya munthuyu yemwe sanali Myuda?
MUTU 98
Anthu a Mitundu Ina Anamva Uthenga Wabwino
Mtumwi Paulo ndi amishonale anzake anayamba kulalikira kumayiko akutali.
MUTU 99
Woyang’anira Ndende Anaphunzira Mawu a Yehova
Zinthu zina zimene zikutchulidwa mu nkhaniyi ndi chiwanda, chivomezi komanso lupanga.
MUTU 101
Paulo Anatumizidwa ku Roma
Ngakhale kuti ulendo wake unali woopsa palibe chilichonse chimene chinalepheretsa mtumwi Paulo pa ulendowo.
MUTU 102
Zimene Yohane Anaona M’masomphenya
Yesu anaonetsa Yohane masomphenya a zimene zidzachitike m’tsogolo.
MUTU 103
“Ufumu Wanu Ubwere”
Zimene Yohane anaona zimasonyeza kuti Ufumu wa Mulungu udzasintha kwambiri zinthu padzikoli.