MUTU 101
Paulo Anatumizidwa ku Roma
Ulendo wachitatu wa Paulo unakathera ku Yerusalemu. Atafika kumeneko anamangidwa. Ndiyeno usiku anaona masomphenya. Yesu anamuuza kuti: ‘Udzapita ku Roma ndipo ukalalikira kumeneko.’ Paulo anatengedwa ku Yerusalemu kupita ku Kaisareya komwe anakakhala m’ndende zaka ziwiri. Pa nthawi imene mlandu wake unkazengedwa ndi bwanamkubwa wina dzina lake Fesito, Paulo ananena kuti: ‘Ndikupempha kuti mlandu wangawu ukaweruzidwe kwa Kaisara.’ Ndiyeno Fesito anati: ‘Poti wapempha kupita kwa Kaisara, upitadi.’ Popita ku Romako Paulo anatengedwa pa sitima yapamadzi ndipo abale awiri, Luka ndi Arisitako, anapita nawo.
Ali panyanja kunachitika chimphepo choopsa kwa masiku ambiri. Aliyense ankaganiza kuti palibe amene apulumuke. Koma Paulo anati: ‘Anthu inu, mngelo wandiuza m’maloto kuti: “Usaope Paulo. Ukafika ku Roma ndipo aliyense musitimayi saafa.” Choncho musachite mantha. Palibe amene afe.’
Chimphepocho chinawomba kwa masiku 14. Kenako anayamba kuona chilumba cha Melita. Koma sitimayo inatitimira mumchenga ndipo inayamba kusweka chifukwa cha mafunde. Ngakhale zinali choncho, anthu onse 276 amene analimo anakafika kumtunda. Ena anasambira pomwe ena anagwiritsa ntchito zidutswa za sitimayo zomwe zinkayandama. Atafika, anthu apachilumbapo anawalandira bwino n’kuwayatsira moto kuti awothe.
Patapita miyezi itatu, asilikali anatenga Paulo pa sitima ina n’kupita naye ku Roma. Atafika, abale anabwera kudzamuona. Paulo atawaona anathokoza Yehova ndipo analimba mtima. Ngakhale kuti anali mkaidi, ankaloledwa kukhala m’nyumba ina ya lendi ndipo ankalonderedwa ndi msilikali. Iye anakhala kumeneko zaka ziwiri. Anthu akabwera kudzamuona, ankawalalikira za Ufumu wa Mulungu komanso za Yesu. Iye analembanso makalata opita kumipingo ya ku Asia Minor ndi ku Yudeya. Apatu Yehova anagwiritsa ntchito Paulo kuti uthenga wabwino ufike kwa anthu a mitundu ina.
“Tikusonyeza mwa njira ina iliyonse kuti ndife atumiki a Mulungu. Tikuchita zimenezi mwa kupirira zambiri, kudutsa m’masautso, kukhala osowa, kukumana ndi zovuta.”—2 Akorinto 6:4