Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 51

Kamtsikana Kanathandiza Mkulu wa Asilikali

Kamtsikana Kanathandiza Mkulu wa Asilikali

Kamtsikana kena ka ku Isiraeli kanatengedwa n’kumakakhala ngati kapolo ku Siriya komwe kunali kutali kwambiri ndi kwawo. Gulu la asilikali a Asuri ndi lomwe linatenga kamtsikanaka. Ku Siriyako kankagwira ntchito kwa mkulu wa asilikali dzina lake Namani. Kamtsikanaka kankalambira Yehova ngakhale kuti anthu a kumeneko ankalambira milungu yabodza.

Namani anali ndi matenda a khate ndipo ankamva ululu kwambiri. Kamtsikanaka kankafunitsitsa kuthandiza Namani. Choncho kanauza abwana ake aakazi kuti: ‘Ndikudziwa munthu amene angathe kuwachiritsa abwanawa. Munthu wake ndi Elisa ndipo amakhala ku Isiraeli. Ndithu angathe kuwachiritsa.’

Mkazi wa Namani anauza mwamuna wake za nkhaniyi. Namani anapitadi ku Isiraeli kuti akaonane ndi Elisa. Atafika kumeneko ankaganiza kuti Elisa amupatsa ulemu wapadera monga munthu wolemekezeka. Koma Elisa sanalankhule naye n’komwe. Anangotumiza mnyamata wake kuti akamulonjere n’kumuuza kuti: ‘Pitani mukasambe maulendo 7 mumtsinje wa Yorodano, mukatero muchira.’

Atamva zimenezi, Namani anakwiya kwambiri. Iye anati: ‘Ndimaganiza kuti mneneri ameneyu andichiritsa poitana dzina la Mulungu wake komanso kuyendetsa dzanja lake uku ndi uku. Ndiye akundiuza kuti ndingopita kumtsinje kukasamba? Kodi sakudziwa kuti ku Siriya kuli mitsinje yoposanso ya ku Isiraeli kuno? Ndiye sindikanatha kungopita kumitsinje ya kwathu komweko?’ Atatero ananyamuka mokhumudwa n’kumapita.

Koma antchito ake anamuthandiza kuti aiganizirenso bwino nkhaniyi. Anamuuza kuti: ‘Kodi simungachite chilichonse chomwe chingathandize kuti muchire? Ndipotu zimene mneneriyu wanenazi si zovuta. Ingochitani zimene wakuuzanizo.’ Namani anamvera antchito akewo ndipo anapita kumtsinje wa Yorodano n’kukasamba ka 7. Atasamba komalizaka anangoona kuti khate lake lonse lija latha. Zitatere anasangalala kwambiri ndipo anapita kwa Elisa kukamuthokoza. Anamuuza kuti: ‘Tsopano ndadziwa kuti Yehova ndi Mulungu woona.’ Kodi ukuganiza kuti kamtsikana kaja kanamva bwanji kataona Namani akubwera atachiritsidwa?

“M’kamwa mwa ana ndi mwa ana oyamwa mwaikamo mawu otamanda.”—Mateyu 21:16