Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 77

Yesu Anakumana ndi Mayi Pachitsime

Yesu Anakumana ndi Mayi Pachitsime

Pasika atatha, Yesu ndi ophunzira ake anayamba ulendo wobwerera ku Galileya ndipo anadutsa ku Samariya. Atafika mumzinda wa Sukari, Yesu anaima pachitsime cha Yakobo. Ophunzira ake anamusiya akupuma, iwo n’kupita kukagula chakudya mumzindawo.

Ndiyeno panafika mayi wina kudzatunga madzi. Yesu anamuuza kuti: “Mundipatseko madzi akumwa mayi.” Mayiyo anati: ‘Bwanji mukupempha madzi kwa ine? Inetu ndine Msamariya. Paja Ayuda salankhula ndi Asamariya.’ Koma Yesu anamuuza kuti: ‘Mukanadziwa kuti ndine ndani, bwenzi mutandipempha kuti ndikupatseni madzi amoyo.’ Mayiyo anafunsa Yesu kuti: ‘Mukutanthauza chiyani? Inu mulibe chotungira ndiye madzi muwatenga kuti?’ Yesu anayankha kuti: ‘Aliyense wakumwa madzi amene ine ndingam’patse sadzamvanso ludzu ngakhale pang’ono.’ Ndiyeno mayiyo anati: “Bambo, ndipatseni madzi amenewo.”

Kenako Yesu anauza mayiyo kuti: ‘Pitani mukaitane mwamuna wanu.’ Koma mayiyo anati: “Ndilibe Mwamuna.” Yesu anati: ‘Mwanena zoona. Pakuti mwakwatiwapo ndi amuna 5, ndipo mwamuna amene mukukhala naye panopa si wanu.’ Mayiyo atamva zimenezi anati: ‘Ndazindikira kuti ndinu mneneri. Ife timakhulupirira kuti tiyenera kulambira Mulungu m’phiri ili, pamene Ayudanu mumati tiyenera kulambira ku Yerusalemu. Koma ndikukhulupirira kuti Mesiya akadzabwera adzatiphunzitsa kuti tizilambira bwanji.’ Ndiyeno Yesu anamuuza zimene anali asanauzepo aliyense. Anati: ‘Ineyo ndine Mesiya.’

Mayiyo anathamanga n’kukauza Asamariya kuti: ‘Ndakumana ndi Mesiya. Akudziwa zonse zokhudza ineyo. Tiyeni mukamuone.’ Anthuwo anapita naye limodzi ndipo Yesu anawaphunzitsa zinthu zambiri.

Asamariyawo anapempha Yesu kuti akhalebe mumzinda wawo. Choncho anakhala nawo kwa masiku awiri n’kumawaphunzitsa ndipo ambiri anamukhulupirira. Iwo anauza mayi uja kuti: ‘Zimene tamva kwa munthuyo zatithandiza kudziwa kuti iyedi ndi mpulumutsi wa dziko.’

“‘Bwera!’ Aliyense wakumva ludzu abwere. Aliyense amene akufuna, amwe madzi a moyo kwaulere.”​—Chivumbulutso 22:17