Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 59

Anyamata 4 Anamvera Yehova

Anyamata 4 Anamvera Yehova

Nebukadinezara atatenga akalonga a ku Yuda n’kupita nawo ku Babulo, anasankha nduna ina dzina lake Asipenazi kuti iziyang’anira akalongawo. Nebukadinezara anauza Asipenazi kuti asankhe anyamata athanzi komanso ooneka bwino. Anamuuza kuti anyamatawo asamaliridwe komanso aphunzitsidwe kwa zaka zitatu n’cholinga choti adzakhale akuluakulu a boma. Anyamata amenewa anayeneranso kuwaphunzitsa kuwerenga, kulemba komanso kulankhula chilankhulo cha Akasidi. Ankafunikanso kumawapatsa chakudya chimene mfumu ndi anthu ogwira ntchito kunyumba yake ankadya. Pagulu la anyamatawa panali Danieli, Hananiya, Misayeli ndi Azariya. Koma Asipenazi anawapatsa mayina achibabulo akuti, Belitesazara, Sadirake, Mesake ndi Abedinego. Kodi zimene ankawaphunzitsazo zinachititsa kuti anyamatawa asiye kutumikira Yehova? Ayi.

Iwo anatsimikiza kuti apitirizabe kumvera Yehova. Ankadziwa kuti sayenera kudya chakudya cha mfumu chifukwa Chilamulo cha Yehova chinkaletsa zina mwa zakudya zimenezo. Choncho anauza Asipenazi kuti: ‘Chonde musamatipatse chakudya cha mfumu.’ Koma Asipenazi anawayankha kuti: ‘Mukapanda kumadya zakudya za mfumu muwonda ndipo mfumu indipha.’

Ndiyeno Danieli anapeza nzeru. Anauza Asipenazi kuti: ‘Mutipatse masamba ndi madzi kwa masiku 10. Kenako mudzayerekeze mmene tikuonekera ndi mmene anyamata ena akuonekera.’ Asipenazi anavomera.

Patatha masiku 10, Danieli ndi anzake atatuwo ankaoneka athanzi kuposa anyamata ena onsewo. Yehova anasangalala chifukwa choti anyamatawa anamumvera ndipo anapatsa Danieli nzeru moti ankatha kudziwa tanthauzo la masomphenya ndi maloto.

Zaka zitatu zija zitatha Asipenazi anapita ndi anyamata onse kwa Nebukadinezara. Iye atalankhula nawo, anaona kuti Danieli, Hananiya, Sadirake ndi Azariya anali anzeru komanso ochangamuka kuposa anyamata enawo. Choncho anawasankha kuti azigwira ntchito kunyumba kwake. Mfumuyi inkafunsira nzeru kwa anyamatawa chifukwa Yehova anawathandiza kukhala ndi nzeru kuposa anzeru onse a m’dzikolo.

Ngakhale kuti anyamata 4 amenewa ankakhala kudziko la eni, sanaiwale kuti iwo anali anthu a Mulungu. Kodi iwenso utakhala kumalo koti kulibe makolo ako, ungapitirizebe kumvera Yehova?

“Usalole kuti munthu aliyense akuderere poona kuti ndiwe wamng’ono. M’malomwake, ukhale chitsanzo kwa okhulupirika m’kalankhulidwe, m’makhalidwe, m’chikondi, m’chikhulupiriro, ndi pa khalidwe loyera.”​—1 Timoteyo 4:12