Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 75

Mdyerekezi Anayesa Yesu

Mdyerekezi Anayesa Yesu

Yesu atabatizidwa mzimu woyera unamutsogolera kupita kuchipululu. Sanadye chilichonse kwa masiku 40 choncho anali ndi njala kwambiri. Ndiyeno Mdyerekezi anabwera kudzamuyesa ndipo anamuuza kuti: ‘Ngati ndinudi Mwana wa Mulungu, uzani miyalayi kuti isanduke mitanda ya mkate.’ Koma Yesu anamuyankha potchula zimene Malemba amanena. Anati: ‘Malemba amanena kuti munthu safunika chakudya chokha kuti akhale ndi moyo. Amafunikanso mawu otuluka pakamwa pa Yehova.’

Kenako Mdyerekezi anauza Yesu kuti: ‘Ngati ndinudi Mwana wa Mulungu, mudumphe kuchokera pamwamba pa kachisi. Pajatu Malemba amanena kuti Mulungu adzatumiza angelo ake kuti adzakunyamuleni kuti musavulale.’ Koma Yesu anayankhanso pogwiritsa ntchito Malemba. Iye anati: ‘Malemba amanena kuti usamuyese Yehova.’

Kenako Mdyerekezi anaonetsa Yesu maufumu onse a padziko lapansi ndi chuma chawo. Ndiyeno anamuuza kuti: ‘Ndikupatsani maufumu onsewa ndi chuma chonsechi ngati mungandiweramireko kamodzi kokha.’ Koma Yesu anayankha kuti: ‘Choka Satana! Malemba amati, uyenera kulambira Yehova yekha basi.’

Yesu atanena zimenezi, Mdyerekezi anamusiya ndipo angelo anabwera n’kudzamupatsa chakudya. Izi zitatha, Yesu anayamba kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Imeneyi ndi ntchito imene Mulungu anamutuma kuti adzachite. Anthu ankakonda zimene Yesu ankaphunzitsa ndipo ankamutsatira kulikonse kumene wapita.

“Pamene [Mdyerekezi] akunena bodza, amalankhula za m’mutu mwake, chifukwa iye ndi wabodza komanso tate wake wa bodza.”​—Yohane 8:44