Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 34

Gidiyoni Anagonjetsa Amidiyani

Gidiyoni Anagonjetsa Amidiyani

Patapita nthawi, Aisiraeli anasiyanso kulambira Yehova ndipo anayamba kulambira milungu yonyenga. Kwa zaka 7, Amidiyani ankaba ziweto za Aisiraeli komanso kuwawonongera mbewu zawo. Pothawa Amidiyaniwo, Aisiraeli ankabisala m’mapanga komanso m’mapiri. Kenako anapempha kuti Yehova awapulumutse. Ndiyeno Yehova anatumiza mngelo kuti apite kwa Gidiyoni. Mngeloyo anauza Gidiyoni kuti: ‘Yehova wakusankha kuti ukhale msilikali wolimba mtima komanso wamphamvu.’ Gidiyoni anafunsa kuti: ‘Kodi munthu wachabechabe ngati ine, ndingapulumutse bwanji Aisiraeli?’

Koma kodi Gidiyoni akanatsimikizira bwanji kuti Yehova anamusankhadi? Iye anaika ubweya pansi n’kumuuza Yehova kuti: ‘Ngati m’mawa, ubweyawu unganyowe ndi mame koma nthaka n’kukhala youma, ndidzadziwa kuti mwandisankhadi kuti ndipulumutse Aisiraeli.’ M’mawa wa tsiku lotsatira anapeza kuti ubweya uja wanyowa koma nthaka ndi youma. Koma Gidiyoni anapemphanso kuti m’mawa wa tsiku lotsatira apeze ubweya uja uli wouma koma nthaka idzakhale yonyowa. Zimenezi zitachitika, Gidiyoni anatsimikizira kuti Yehova anamusankhadi. Ndiyeno anasonkhanitsa asilikali ake kuti akamenyane ndi Amidiyani.

Yehova anauza Gidiyoni kuti: ‘Ndithandiza Aisiraeli kuti apambane pa nkhondoyi. Koma chifukwa uli ndi asilikali ambiri, ungaganize kuti mwapambana ndi mphamvu zanu. Uza aliyense amene akuchita mantha kuti abwerere.’ Choncho asilikali 22,000 anabwerera n’kutsala okwana 10,000. Yehova ananena kuti: ‘Asilikaliwa achulukabe. Pita nawo kumtsinje ndipo ukawauze kuti akamwe madzi. Ndiyeno ukasankhe omwe azikamwa madzi, uku akuyang’ana adani awo.’ Asilikali 300 okha ndi amene anali tcheru pamene ankamwa. Yehova analonjeza kuti asilikali ochepawo adzagonjetsa asilikali a Amidiyani okwana 135,000.

Usiku, Yehova anauza Gidiyoni kuti: ‘Tsopano pitani mukamenyane ndi Amidiyani. Gidiyoni anapatsa asilikali akewo malipenga a nyanga ndi mitsuko ikuluikulu ndipo m’mitsukomo anaikamo miyuni. Iye anawauza kuti: ‘Muzionetsetsa zimene ndikuchita ndipo nanunso muzichita zomwezo.’ Gidiyoni analiza lipenga lake, n’kuphwanya mtsuko uja ndiyeno ananyamula muuni wake m’mwamba n’kufuula kuti: ‘Nkhondo ya Yehova ndi ya Gidiyoni!’ Asilikali 300 aja anachitanso chimodzimodzi. Amidiyani atamva zimenezi anachita mantha ndipo anayamba kuthawa. Chifukwa chosokonezeka, iwo anayamba kuukirana okhaokha. Apa Yehova anathandiza Aisiraeli kugonjetsa adani awo.

“Mphamvu yoposa yachibadwa ichokere kwa Mulungu, osati kwa ife.”​—2 Akorinto 4:7