Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 7

Nsanja ya ku Babele

Nsanja ya ku Babele

Chigumula chitatha, ana a Nowa anabereka ana ambiri. Choncho anayamba kukhala m’madera osiyanasiyana padziko lapansi. Izi ndi zimene Yehova anawauza.

Koma anthu ena sanamvere Yehova. Iwo anauzana kuti: ‘Tiyeni timange mzinda kuti tizingokhala pompano. Timange nsanja yaitali yoti mpaka ikafike kumwamba. Tikatero titchuka.’

Yehova sanasangalale ndi zimene anthuwa ankachita ndipo anaganiza zowaletsa. Kodi ukudziwa zimene anachita? Anachititsa kuti mwadzidzidzi anthuwo ayambe kulankhula zinenero zosiyanasiyana. Popeza sankathanso kumvana, anasiya ntchito yomangayo. Mzinda umene ankamangawo unatchedwa Babele kutanthauza “Chisokonezo.” Ndiyeno anthuwo anayamba kubalalikana. Koma anapitirizabe kuchita zoipa m’madera osiyanasiyana amene ankakhala. Kodi panali ena amene ankakonda Yehova? Tikambirana zimenezi m’mutu wotsatira.

“Aliyense wodzikweza adzam’nyazitsa, koma wodzichepetsa adzamukweza.”​—Luka 18:14