Mawu Ofotokoza Chigawo 3
Baibulo limanena kuti Chigumula chitatha, panali anthu ena omwe ankatumikira Yehova. Ena mwa anthuwa anali Abulahamu amene ankadziwika kuti anali mnzake wa Yehova. N’chifukwa chiyani Abulahamu ankatchedwa mnzake wa Yehova? Ngati ndinu kholo, thandizani mwana wanu kudziwa kuti Yehova amamukonda kwambiri ndipo amafunitsitsa kumuthandiza. Mofanana ndi Abulahamu komanso anthu ena okhulupirika monga Loti ndi Yakobo, tingathe kupempha Yehova kuti atithandize. Komanso tizikhulupirira kuti Yehova adzachita chilichonse chimene wanena.
M'CHIGAWO ICHI
MUTU 7
Nsanja ya ku Babele
Anthu anaganiza zomanga mzinda wokhala ndi nsanja yaitali mpaka kumwamba. N’chifukwa chiyani Mulungu anawapangitsa kuti mwadzidzidzi ayambe kulankhula zinenero zosiyanasiyana?
MUTU 8
Abulahamu ndi Sara Anamvera Mulungu
N’chifukwa chiyani Abulahamu ndi Sara anasiya mzinda wolemera wa Uri n’kumakakhala ngati alendo ku Kanani?
MUTU 9
Anakhala Ndi Mwana Atakalamba
Kodi Mulungu anakwaniritsa bwanji lonjezo lake kwa Abulahamu? Kodi analikwaniritsa kudzera mwa mwana uti, Isaki kapena Isimaeli?
MUTU 10
Kumbukirani Mkazi wa Loti
Mulungu anachititsa kuti moto ndi sulufule zigwere mumzinda wa Sodomu ndi wa Gomora. N’chifukwa chiyani mizindayi inawonongedwa? N’chifukwa chiyani tiyenera kukumbukira mkazi wa Loti?
MUTU 11
Abulahamu Anasonyeza Kuti Anali Wokhulupirika
Mulungu anauza Abulahamu kuti: ‘Chonde, tenga mwana wako mmodzi yekhayo kuti ukamupereke nsembe paphiri la Moriya.’ Kodi pamenepa Abulahamu akanatani?
MUTU 12
Yakobo Analandira Madalitso
Isaki ndi Rebeka anali ndi ana awiri amapasa ndipo mayina awo anali Esau ndi Yakobo. Esau anali wamkulu ndipo ankayenera kulandira madalitso. N’chifukwa chiyani anasinthanitsa madalitsowo ndi mbale ya mphodza?
MUTU 13
Yakobo ndi Esau Anagwirizananso
Kodi Yakobo anatani kuti mngelo amudalitse? Nanga anatani kuti akhululukirane ndi Esau?