Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 96

Yesu Anasankha Saulo

Yesu Anasankha Saulo

Saulo anali Mroma ndipo anabadwira ku Tariso. Iye anali Mfarisi ndipo ankadziwa bwino Chilamulo cha Mose koma ankadana kwambiri ndi Akhristu. Ankawagwira n’kupita nawo kundende. Iye analiponso pamene anthu olusa ankagenda Sitefano ndi miyaya mpaka kumupha.

Koma Saulo sanakhutire ndi kumanga Akhristu ku Yerusalemu. Choncho anapempha chilolezo kwa mkulu wa ansembe kuti akagwirenso Akhristu a mumzinda wa Damasiko. Koma atatsala pang’ono kufika mumzindawo, mwadzidzidzi anaona kuwala ndipo anagwa pansi. Kenako anamva mawu akuti: ‘Saulo, kodi ukundizunziranji?’ Iye anafunsa kuti: ‘Ndinu ndani?’ Mawu aja anamvekanso kuti: ‘Ndine Yesu. Pita ku Damasiko ndipo ukauzidwa zoyenera kuchita.’ Nthawi yomweyo Saulo anakhala wakhungu moti anachita kumugwira dzanja n’kumamutsogolera.

Ku Damasiko kunali Mkhristu wina wokhulupirika dzina lake Hananiya. Yesu anauza Hananiya kuti: ‘Pita ku Msewu Wowongoka ndipo ukafike panyumba ya Yudasi n’kufunsa za munthu wotchedwa Saulo.’ Koma Hananiya anati: ‘Ambuye, munthu ameneyo ndikumudziwa bwino. Akumagwira ophunzira n’kumawatsekera m’ndende.’ Yesu anati: ‘Pita. Ndasankha Saulo kuti azilalikira uthenga wabwino kwa anthu a mitundu yambiri.’

Hananiya anapitadi ndipo atapeza Saulo anamuuza kuti: ‘M’bale wanga Saulo, Yesu wandituma kuti ndidzatsegule maso ako.’ Nthawi yomweyo Saulo anayamba kuona. Anadziwa za Yesu ndipo anakhala wophunzira wake. Atabatizidwa anayamba kulalikira m’masunagoge. Ayuda anadabwa kwambiri ataona kuti Saulo wayamba kuphunzitsa anthu za Yesu. Iwo anati: ‘Si munthu amene ankagwira ophunzira a Yesu uja uyu?’

Saulo anaphunzitsa anthu a ku Damasiko kwa zaka zitatu. Koma Ayuda ankadana naye kwambiri ndipo anakonza zoti amuphe. Abale atamva zimenezi anamuika m’dengu n’kumutulutsira pawindo la mpanda.

Saulo atafika ku Yerusalemu, anafuna kuti azikhala limodzi ndi abale. Koma abalewo ankamuopa. Kenako wophunzira wina wotchedwa Baranaba anamukomera mtima ndipo anapita naye kwa atumwi n’kuwafotokozera kuti Sauloyo anasintha kwambiri ndipo tsopano ndi Mkhristu. Saulo anayamba kulalikira molimba mtima limodzi ndi mpingo wa ku Yerusalemu. Kenako anayamba kudziwika ndi dzina lakuti Paulo.

“Khristu Yesu anabwera m’dziko kudzapulumutsa ochimwa . . . Mwa ochimwa amenewa, ine ndiye wochimwa kwambiri.”​—1 Timoteyo 1:15