Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mawu Ofotokoza Chigawo cha 8

Mawu Ofotokoza Chigawo cha 8

Yehova anadalitsa Solomo pomupatsa nzeru komanso mwayi woti adzamange kachisi. Koma patapita nthawi Solomo anasiya kulambira Yehova. Ngati ndinu kholo, fotokozerani mwana wanu zimene zinachititsa kuti Solomo asiye kulambira Yehova. Ufumu wa Isiraeli unagawikana ndipo mafumu oipa anachititsa kuti anthu asiye kulambira Mulungu n’kumalambira mafano. Pa nthawi imeneyo, atumiki ambiri a Yehova ankazunzidwa kapenanso kuphedwa kumene. Mfumukazi Yezebeli inachititsa kuti anthu a mu ufumu wakumpoto azilambira kwambiri mafano. Imeneyi inali nthawi yovuta kwambiri kwa Aisiraeli. Komabe panali anthu ena amene ankatumikira Yehova mokhulupirika. Ena mwa anthuwa anali Mfumu Yehosafati komanso mneneri Eliya.

M'CHIGAWO ICHI

MUTU 44

Kachisi wa Yehova

Mulungu anayankha pemphero la Solomo ndipo anamupatsa zinthu zambiri.

MUTU 45

Ufumu Unagawikana

Aisiraeli ambiri anasiya kutumikira Yehova

MUTU 46

Zimene Zinachitika Paphiri la Karimeli

Kodi Mulungu woona ndi ndani? Yehova kapena Baala?

MUTU 47

Yehova Analimbikitsa Eliya

Kodi mukuganiza kuti nanunso angakulimbikitseni?

MUTU 48

Mwana wa Mzimayi Wamasiye Anaukitsidwa

M’nyumba mwa mzimayi wamasiye munachitika zozizwitsa ziwiri

MUTU 49

Yehova Anapereka Chilango kwa Mfumukazi Yoipa

Yezebeli anakonza zoti Mwisiraeli wotchedwa Naboti aphedwe n’cholinga choti alande munda wake. Koma Yehova Mulungu anaona zinthu zopanda chilungamozi

MUTU 50

Yehova Anathandiza Mfumu Yehosafati

Yehosafati anali mfumu yabwino ndipo adani ataukira Yuda, iye anapemphera kwa Mulungu kuti amuthandize.