Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 90

Yesu Anaphedwa ku Gologota

Yesu Anaphedwa ku Gologota

Ansembe aakulu anatenga Yesu kupita naye kwa bwanamkubwa wina dzina lake Pilato. Pilatoyo anafunsa anthuwo kuti: ‘Kodi munthuyu walakwa chiyani?’ Iwo anayankha kuti: ‘Akunena kuti ndi mfumu yathu.’ Ndiyeno Pilato anafunsa Yesu kuti: ‘Kodi ndiwe Mfumu ya Ayuda?’ Yesu anayankha kuti: ‘Ufumu wanga si wapadzikoli.’

Zitatero, Pilato anatumiza Yesu kwa Herode, amene anali wolamulira chigawo cha Galileya, kuti akaone ngati Yesuyo alidi ndi mlandu. Koma Herode anapeza kuti Yesu sanalakwe chilichonse. Choncho anamubwezeranso kwa Pilato. Ndiyeno Pilato anauza anthuwo kuti: ‘Ine ndi Herode taona kuti munthuyu ndi wosalakwa. Choncho ndimumasula.’ Koma anthuwo anakuwa kuti: ‘Mupheni! Mupheni!’ Asilikali anayamba kukwapula Yesu, kumulavulira komanso kumumenya. Anamuvekanso chipewa chaminga n’kumamunyoza kuti: ‘Muli bwanji Mfumu ya Ayuda?’ Pilato anauzanso anthuwo kuti: ‘Ine sindinapeze mlandu uliwonse pa munthuyu.’ Koma anthuwo anakuwanso kuti: “Apachikidwe ameneyo!” Choncho Pilato anawapatsa Yesu kuti akamupachike.

Ndiyeno anapita naye kumalo otchedwa Gologota ndipo anakamukhomerera pamtengo n’kuimika mtengowo. Koma Yesu anapemphera kuti: ‘Atate, muwakhululukire chifukwa sakudziwa zimene akuchita.’ Anthu anayamba kunyoza Yesu n’kumanena kuti: ‘Ngati ndiwe Mwana wa Mulungu, tsika pamtengopo. Dzipulumutse.’

Wachifwamba wina amene anapachikidwa pafupi ndi Yesu anamuuza kuti: “Mukandikumbukire mukakalowa mu ufumu wanu.” Atatero, Yesu anamulonjeza kuti: “Udzakhala ndi ine m’Paradaiso.” Masana kunagwa mdima kwa maola atatu. Mayi ake komanso ophunzira ake ena anali chapafupi. Yesu anauza Yohane kuti azisamalira Mariya ngati mayi ake enieni.

Kenako Yesu anauza Mulungu kuti: “Ndakwaniritsa chifuniro chanu!” Ndiyeno anaweramira pansi ndipo anamwalira. Pa nthawi imeneyo panachitika chivomerezi champhamvu. Komanso chinsalu cha m’kachisi chomwe chinkasiyanitsa Malo Oyera ndi Malo Oyera Koposa chinang’ambika pakati. Mkulu wa asilikali ataona zimenezi anati: ‘Uyu analidi Mwana wa Mulungu.’

“Malonjezo a Mulungu, kaya akhale ochuluka chotani, akhala Inde kudzera mwa iye.”​—2 Akorinto 1:20