Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 66

Ezara Ankaphunzitsa Chilamulo cha Mulungu

Ezara Ankaphunzitsa Chilamulo cha Mulungu

Panali patatha zaka 70 kuchokera pamene Aisiraeli anabwerera ku Yerusalemu. Komabe panali Aisiraeli ena amene ankakhalabe madera ena a mu ufumu wa Perisiya. Mmodzi mwa anthu amenewa anali Ezara ndipo ankaphunzitsa anthu Chilamulo cha Yehova. Ezara anamva kuti Aisiraeli ena amene ankakhala ku Yerusalemu sankatsatira Chilamulo. Choncho anaganiza zopita kuti akawathandize. Mfumu Aritasasita anamuuza kuti: ‘Mulungu anakupatsa nzeru kuti uziphunzitsa Chilamulo chake. Pita ku Yerusalemu ndipo ungathe kutenga aliyense amene akufuna kupita nawe.’ Ezara anakumana ndi onse amene ankafuna kubwerera ku Yerusalemu. Iwo anapemphera kwa Yehova kuti awathandize kuti ayende bwino pa ulendowu ndipo kenako ananyamuka.

Patatha miyezi 4 anafika ku Yerusalemu. Akalonga anauza Ezara kuti: ‘Aisiraeli asiya kumvera Yehova ndipo akwatira akazi olambira milungu yonama.’ Ndiye kodi Ezara anatani? Iye anagwada pamaso pa anthu onse n’kupemphera kuti: ‘Yehova, mwatichitira zambiri, koma ifeyo takuchimwirani.’ Anthuwo analapa koma panali zinthu zina zolakwika zomwe ankafunika kukonza. Choncho Ezara anasankha akulu ndi oweruza kuti athandize anthuwo. Mmene pankatha miyezi itatu n’kuti anthu onse amene sankalambira Yehova atathamangitsidwa.

Tsopano zaka 12 zinadutsa. Pa nthawiyi Aisiraeli anamanganso mpanda wa Yerusalemu. Choncho anasonkhanitsa anthu n’kuyamba kuwawerengera Chilamulo cha Mulungu. Ezara atangotsegula buku la Chilamulo, anthu onse anaimirira. Iye anatamanda Yehova ndipo nawonso anthuwo anakweza manja potamanda Yehova. Kenako Ezara anayamba kuwerenga Chilamulocho ndipo anthuwo ankamvetsera mwatcheru. Iwo anavomereza kuti anali atasiya kulambira Yehova ndipo analira. Tsiku lotsatira Ezara anapitiriza kuwawerengera Chilamulocho. Anthuwa anazindikira kuti ankafunika kuchita Chikondwerero cha Misasa ndipo nthawi yomweyo anayamba kukonzekera.

Aisiraeli anachita chikondwererochi kwa masiku 7 ndipo anasangalala komanso anathokoza Yehova powapatsa zokolola zambiri. Panali pasanachitike Chikondwerero cha Misasa ngati chimenechi kuyambira m’nthawi ya Yoswa. Chikondwererochi chitatha, anthuwo anasonkhana n’kupemphera kuti: ‘Yehova, munatipulumutsa ku ukapolo, munatidyetsa m’chipululu komanso munatipatsa dziko lokongola. Koma ifeyo takhala tikukuchimwirani mobwerezabwereza. Munatitumizira aneneri koma sitinanawamvere. Komabe munatilezera mtima ndipo munasunga lonjezo lanu kwa Abulahamu. Tsopano tikukulonjezani kuti tizikumverani.’ Atatero analemba lonjezo lawolo ndipo akalonga, Alevi komanso ansembe anatsimikiza lonjezolo ndi chidindo chawo.

“Odala ndi amene akumva mawu a Mulungu ndi kuwasunga!”​—Luka 11:28