MUTU 83
Yesu Anadyetsa Anthu Ambiri
Tsiku lina atumwi anabwera kuchokera kumene ankalalikira. Apa n’kuti Pasika wa mu 32 C.E. atangotsala pang’ono kufika. Atumwiwo anali atatopa kwambiri ndipo Yesu ananyamuka nawo pa boti kupita ku Betsaida kuti akapume. Koma atayandikira kumtunda anaona kuti anthu ambirimbiri afika kale ndipo akuwadikira. Ngakhale kuti inali nthawi yoti apume ndi ophunzira ake, Yesu anawalandira bwino. Anachiritsa odwala onse ndipo kenako anayamba kuwaphunzitsa. Yesu anawaphunzitsa za Ufumu wa Mulungu tsiku lonse. Ndiyeno madzulo, atumwi anamuuza kuti: ‘Anthuwatu ali ndi njala. Auzeni azipita kuti akapeze chakudya.’
Yesu anayankha kuti: ‘Asapite. Inuyo muwapatse chakudya.’ Atumwiwo anafunsa kuti: ‘Mukutanthauza kuti tipite kukawagulira chakudya?’ Ndiyeno mtumwi wina dzina lake Filipo anati: ‘Ngakhale tikanakhala ndi ndalama zambiri sitingakwanitse kugula chakudya cha anthu onsewa.’
Yesu anawafunsa kuti: ‘Chakudya chomwe tili nacho n’chochuluka bwanji?’ Andireya anati: ‘N’chochepa kwambiri. Tili ndi mikate 5 ndi nsomba ziwiri basi.’ Kenako Yesu anati: ‘Bweretsani.’ Ndiyeno anauza anthuwo kuti akhale pa udzu m’magulu a anthu 50 kapena 100. Yesu anatenga mikate ndi nsombazo n’kuyang’ana kumwamba ndipo anapemphera. Kenako anapereka chakudyacho kwa ophunzira ake ndipo ophunzirawo ankapereka kwa anthu. Panali amuna 5,000 ndiponso akazi ndi ana koma onse anadya n’kukhuta. Atumwiwo anatolera zotsalira n’cholinga choti pasatayidwe
kalikonse. Zotsalazo zinakwana mabasiketi 12. Izitu zinali zodabwitsa kwambiri.Anthu ataona zimenezi anadabwa kwambiri moti ankafuna kuti Yesu akhale mfumu yawo. Koma Yesu anadziwa kuti imeneyo sinali nthawi imene Yehova ankafuna kuti iye akhale mfumu. Kenako anauza anthu onse kuti azipita ndipo iye ndi atumwi ake anapita tsidya lina la nyanja ya Galileya. Atumwiwo anakwera boti koma Yesu anapita yekha kuphiri kuti akapemphere kwa Atate wake. Yesu ankayesetsa kupeza mpata wopemphera ngakhale kuti ankatanganidwa kwambiri.
“Musamagwire ntchito kuti mungopeza chakudya chimene chimawonongeka, koma kuti mupeze chakudya chokhalitsa, chopereka moyo wosatha, chimene Mwana wa munthu adzakupatsani.”—Yohane 6:27