Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 28

Bulu wa Balamu Analankhula

Bulu wa Balamu Analankhula

Aisiraeli atakhala m’chipululu zaka pafupifupi 40, anagonjetsa mizinda yambiri yamphamvu. Kenako anamanga misasa yawo m’chipululu cha Mowabu chakum’mawa kwa mtsinje wa Yorodano. Nthawi yoti alowe m’dziko lolonjezedwa inali itakwana. Ndiyeno mfumu ya Mowabu dzina lake Balaki anaopa kwambiri podziwa kuti dziko lake ligonjetsedwa. Choncho anaitanitsa munthu wina dzina lake Balamu kuti adzatemberere Aisiraeli.

Koma Yehova anauza Balamu kuti: ‘Iwe, usakatemberere Aisiraeli.’ Choncho Balamu anakana kupita ku Mowabu. Mfumu ija inamuitananso kachiwiri n’kumulonjeza kuti imupatsa chilichonse chimene angafune. Koma Balamu anakanabe. Kenako Mulungu anamuuza kuti: ‘Ukhoza kupita koma ukanene zimene ndingakuuze zokhazokha.’

Ndiyeno Balamu ananyamuka pa bulu wake kupita ku Mowabu. Mumtima mwake ankafuna kukatembereradi Aisiraeli ngakhale kuti Yehova anamuuza kuti asakachite zimenezo. Ndiyeno mngelo wa Yehova anakumana naye katatu panjira imene anadutsayo. Balamu sankaona mngeloyu koma bulu wake ankamuona. Ulendo woyamba, buluyo anapatuka n’kudutsa m’munda. Kachiwiri buluyo anapatukanso n’kudutsa pafupi ndi mpanda moti anakanikizira phazi la Balamu kukhoma. Kachitatu, buluyo anangogona pakati pa msewu. Maulendo onsewa Balamu ankamenya buluyo ndi ndodo.

Ndiyeno ulendo wachitatuwu, Yehova anachititsa kuti buluyo alankhule. Buluyo anafunsa Balamu kuti: ‘Kodi iwe ukundimenyeranji?’ Balamu anamuyankha kuti: ‘Chifukwa ukundipusitsa, ndipo mwayi kuti ndilibe lupanga. Ndikanakupha.’ Buluyo anati: ‘Ndakhala ndikuyenda nawe kwa zaka zambirimbiri. Kodi ndinayamba ndachitapo zimenezi?’

Kenako Yehova anachititsa Balamu kuti aone mngeloyo. Ndiyeno mngeloyo anati: ‘Kodi Yehova sanakuuze kuti usakatemberere Aisiraeli?’ Balamu anayankha kuti: ‘Pepani ndalakwa. Ndibwerera.’ Koma mngeloyo  anati: ‘Pita ku Mowabu koma uzikanena zimene Yehova angakuuze zokhazokha.’

Balamu sanaphunzirepo kanthu. Iye anayesa kutemberera Aisiraeli maulendo atatu. Koma Yehova anamuchititsa kuti awadalitse m’malo mowatemberera. Kenako, Aisiraeli anagonjetsa dziko la Mowabu ndipo Balamu anaphedwa. Iye akanamvera Yehova, zikanamuyendera bwino.

“Chenjerani ndi kusirira kwa nsanje kwamtundu uliwonse, chifukwa ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.”​—Luka 12:15