Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 54

Yehova Anamulezera Mtima Yona

Yehova Anamulezera Mtima Yona

Anthu a mumzinda wa Nineve ankachita zinthu zoipa. Choncho Yehova anauza mneneri wake Yona kuti apite kukawachenjeza kuti asiye zoipazo. Koma Yona anathawa ndipo anakwera sitima yapamadzi yopita ku Tarisi.

Ali pa ulendowu, panyanja panayamba chimphepo champhamvu moti oyendetsa sitima anachita mantha kwambiri. Iwo anapemphera kwa milungu yawo n’kumafunsa kuti: ‘Kodi izi zikuchitika chifukwa chiyani?’ Kenako Yona anawauza kuti: ‘Anthuni, wolakwa ndine. Yehova anandiuza kuti ndichite zinazake ndiye ndikuthawa. Mundiponye m’nyanjamu ndipo mphepoyi isiya.’ Oyendetsa sitimawo sankafuna kumuponya m’madzi koma Yona analimbikira kuti amuponye. Kenako anamuponyadi ndipo mphepo ija inasiyira pomwepo.

Yona ankangoganiza kuti afa basi. Pamene ankamira, anayamba kupemphera kwa Yehova. Zitatero, Yehova anatumiza chinsomba chimene chinameza Yona. Komabe iye sanafe. Ali m’mimba mwa chinsombacho anapempheranso kuti: ‘Yehova, ndikukulonjezani kuti ndizimvera chilichonse chimene mungandiuze.’ Yona anakhala m’mimba mwa chinsombacho kwa masiku atatu ndipo kenako chinakamulavulira kumtunda.

Yona atapulumuka, Yehova anamuuzanso kuti apite ku Nineve kuja. Pa nthawiyi Yona sanakane. Atafika kumeneko anauza anthu oipawo kuti: ‘Kwangotsala masiku 40 ndipo mzinda wa Nineve uwonongedwa.’ Anthu a ku Nineve anatamva uthengawo anasinthiratu. Mfumu yawo inalamula kuti:  ‘Tiyeni tipemphere kwa Mulungu ndipo tisiye zoipa. Mwina satiwononga.’ Yehova ataona kuti anthuwo alapa, sanawononge mzindawo.

Izi si zimene Yona ankayembekezera choncho anakwiya kwambiri. Ndiye tangoganiza, Yehova analezera mtima Yona komanso kumuchitira chifundo, koma iyeyo sanachitire chifundo anthu a ku Nineve. Yona anangotuluka mumzindawo n’kukakhala pansi pa kamtengo. Kenako kamtengoko kanauma ndipo Yona anakwiyanso. Ndiyeno Yehova anamufunsa kuti: ‘Kodi ukumvera chisoni mtengowu koma osamvera chisoni anthu a ku Nineve? Inetu ndawachitira chifundo ndipo sindinawawononge.’ Kodi Yehova ankatanthauza chiyani pamenepa? Ankatanthauza kuti anthu a ku Nineve anali ofunika kuposa mtengo uliwonse.

“Yehova . . . akuleza nanu mtima, pakuti safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.”​—2 Petulo 3:9