Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 99

Woyang’anira Ndende Anaphunzira Mawu a Yehova

Woyang’anira Ndende Anaphunzira Mawu a Yehova

Ku Filipi kunali mtsikana wina wantchito amene anali ndi chiwanda. Chiwandacho chinkachititsa mtsikanayo kuti azineneratu zam’tsogolo ndipo ankalemeretsa mabwana ake. Ndiyeno Paulo ndi Sila atafika ku Filipiko, mtsikanayo ankawatsatira kwa masiku ambiri. Chiwandacho chinkamuchititsa kufuula kuti: “Anthu awa ndi akapolo a Mulungu Wam’mwambamwamba!” Paulo atatopa nazo anauza chiwandacho kuti: “Ndikukulamula m’dzina la Yesu Khristu kuti utuluke mwa mtsikanayu!” Nthawi yomweyo chiwandacho chinamusiya.

Mabwana a mtsikanayu ataona kuti mwayi wawo wopeza ndalama watha, anakwiya kwambiri. Iwo anagwira Paulo ndi Sila n’kuwakokera kubwalo la olamulira ndipo anati: ‘Anthu awa akuphwanya malamulo ndipo akusokoneza kwambiri mzindawu.’ Ndiyeno akuluakulu a boma analamula kuti Paulo ndi Sila akwapulidwe kenako atsekeredwe m’ndende. Anawaika m’ndende yamdima ndipo anawamangirira m’matangadza.

M’ndendemo, Paulo ndi Sila ankaimba nyimbo zotamanda Mulungu ndipo akaidi ena ankamvetsera. Ndiyeno pakati pa usiku, kunachitika chivomezi chomwe chinagwedeza kwambiri ndendeyo. Zitseko zonse zinatseguka ndipo maunyolo a akaidi onse anamasuka. Woyang’anira ndende uja atathamanga n’kupeza kuti zitseko zatseguka anaganiza kuti akaidi onse athawa. Choncho anatenga lupanga kuti adziphe.

Koma Paulo anamuuza kuti: ‘Usadzivulaze! Tonse tili mommuno!’ Woyang’anira ndendeyo analowa msanga n’kugwada pafupi ndi Paulo ndi Sila. Kenako anafunsa kuti: ‘Ndichite chiyani kuti ndidzapulumuke?’ Iwo anamuyankha kuti: ‘Iweyo ndi banja lako muyenera kukhulupirira Yesu.’ Kenako Paulo ndi Sila anayamba kuphunzitsa woyang’anira ndendeyo ndi banja lake Mawu a Yehova ndipo onse anabatizidwa.

“Anthu adzakugwirani ndi kukuzunzani, adzakuperekani kumasunagoge ndi kundende. Adzakutengerani kwa mafumu ndi abwanamkubwa chifukwa cha dzina langa. Umenewu udzakhala mpata wanu wochitira umboni.”​—Luka 21:12, 13