MUTU 86
Yesu Anaukitsa Lazaro
Yesu anali ndi anzake atatu amene ankakhala ku Betaniya. Anzakewo anali Lazaro ndi azichemwali ake awiri, Mariya ndi Marita. Tsiku lina, Yesu ali kutsidya lina la Yorodano, Mariya ndi Marita anamutumizira uthenga wakuti: ‘Lazaro akudwala mwakayakaya. Chonde mubwere mwamsanga.’ Koma Yesu sanapite nthawi yomweyo. Anakhalabe masiku awiri kenako anauza ophunzira ake kuti: ‘Tiyeni ku Betaniya. Lazaro akugona ndiye ndikufuna ndikamudzutse.’ Atumwiwo anati: ‘Ngati Lazaroyo akugona zimuthandiza kuti apeze bwino mwamsanga.’ Apa tsopano Yesu anawauza kuti: ‘Lazaro wamwalira.’
Pamene Yesu ankafika ku Betaniya n’kuti Lazaro atakhala m’manda masiku 4. Kunali anthu ambiri amene anabwera kudzatonthoza Marita ndi Mariya. Marita atamva kuti Yesu akubwera, anamuchingamira ndipo atakumana naye anati: ‘Ambuye, mukanakhala kuno mchimwene wanga sakanamwalira.’ Yesu anamuyankha kuti: ‘Mchimwene wako adzauka. Ukukhulupirira zimenezo?’ Marita anati: ‘Eya, ndikukhulupirira kuti adzauka pa tsiku lomaliza.’ Ndiyeno Yesu anati: ‘Ine ndine kuuka ndi moyo.’
Kenako Marita anapita kukauza Mariya kuti: ‘Yesu wabwera.’ Mariya anathamangira kwa Yesu ndipo gulu la anthu linamutsatira. Mariya anagwada pafupi ndi Yesu ndipo ankangolira. Kenako anati: ‘Ambuye, mukanakhala kunotu mchimwene wathu sakanamwalira.’ Yesu ataona kuti Mariya ali ndi chisoni kwambiri, nayenso anayamba kulira. Anthu ataona kuti Yesu akugwetsa misozi anati: ‘Eee, koma ndiye ankamukonda kwambiri Lazaro.’ Koma ena anayamba kufunsa kuti: ‘Ndiye n’chifukwa chiyani sanamuthandize kuti asafe?’ Kodi Yesu anatani?
Yesu ndi anthuwo anapita kumanda ndipo anapeza kuti pamandapo atsekapo ndi chimwala. Iye anauza anthu kuti: ‘Chotsani chimwalachi.’ Koma Marita anati: ‘Wakhalatu m’manda kwa masiku 4. Ayenera kuti wayamba kununkha.’ Koma anthu anachotsabe mwalawo ndipo Yesu anapemphera kuti: ‘Atate, ndikuthokoza kuti mwandimva. Ndikudziwa kuti mumandimva nthawi zonse, koma ndikupemphera mokweza chonchi kuti
anthuwa adziwe zoti inuyo munanditumiza.’ Kenako anafuula kuti: “Lazaro, tuluka!” Atatero panachitika zodabwitsa. Lazaro uja anatuluka adakali munsalu zimene anamukulungamo. Yesu anati: “M’masuleni ndi kumuleka apite.”Anthu ambiri amene anaona zimenezi anakhulupirira Yesu. Koma ena anapita n’kukauza Afarisi ndipo Afarisiwo anayamba kufuna kupha Lazaro ndi Yesu. Mmodzi mwa atumwi 12 aja dzina lake Yudasi, anazemba n’kupita kwa Afarisi kukawauza kuti: ‘Mundipatsa ndalama zingati ndikakuthandizani kupeza Yesu?’ Anagwirizana naye kuti amupatsa ndalama 30 zasiliva. Choncho Yudasi anayamba kufufuza mpata woti apereke Yesu.
“Mulungu woona ndi Mulungu amene amatipulumutsa. Ndipo njira zopulumukira ku imfa ndi za Yehova Ambuye Wamkulu Koposa.”—Salimo 68:20