MUTU 15
Yehova Sanamuiwale Yosefe
Yosefe ali m’ndende, Farao yemwe anali mfumu ya ku Iguputo, analota maloto. Palibe amene ankadziwa tanthauzo la malotowo. Wantchito wina wa Farao ananena kuti Yosefe akhoza kufotokoza tanthauzo lake. Nthawi yomweyo, Farao anaitanitsa Yosefe.
Atafika, Farao anamufunsa kuti: ‘Kodi ungandiuze tanthauzo la maloto anga?’ Yosefe anayankha kuti: ‘Pa zaka 7 zikubwerazi, mu Iguputo muno mukhala zakudya zambirimbiri koma kenako kudzabwera zaka zina 7 za njala. Musankhe munthu wanzeru kuti asonkhanitse chakudya kuti anthu anu asadzafe ndi njala.’ Farao anayankha kuti: ‘Ndakusankha iweyo. Ukhala wachiwiri wanga.’ Kodi Yosefe anadziwa bwanji tanthauzo la maloto a Farao? Yehova ndi amene anamuthandiza.
Ndiyeno Yosefe anasonkhanitsa chakudya kwa zaka 7. Kenako padziko lonse panali njala ngati mmene iye ananenera. Anthu ochokera m’mayiko osiyanasiyana ankabwera kudzagula chakudya kwa Yosefe. Ndiyeno bambo ake atamva kuti ku Iguputo kuli chakudya, anatuma ana awo 10 kuti apite kukagula chakudya.
Ana a Yakobo anapita kwa Yosefe ndipo iye atangowaona anawazindikira. Koma azichimwene akewo sanamuzindikire. Iwo anamugwadira ndipo izi zinali zogwirizana ndi maloto amene Yosefe analota ali wamng’ono. Koma iye ankafuna kudziwa ngati abale akewo adakali ndi chidani. Choncho anawauza kuti: ‘Inu ndinu akazitape! Mwabwera kuno kudzafufuza malo amene dziko lathu lili lofooka.’ Iwo anayankha kuti: ‘Ayi ndithu. Tachokera ku Kanani ndipo m’banja lathu tinalimo amuna 12. M’bale wathu wina anamwalira ndipo wamng’ono watsala ndi bambo athu.’ Kenako Yosefe
anati: ‘Mukabwere ndi mng’ono wanuyo kuti ndikukhulupirireni.’ Zitatero azichimwene ake a Yosefewo anabwerera kwawo.Ndiyeno chakudya chija chitatha, Yakobo anauza ana akewo kuti apitenso ku Iguputo. Pa ulendowu anatenga mng’ono wawo uja ndipo dzina lake linali Benjamini. Pofuna kuwayesa abale akewo, Yosefe anabisa kapu yake m’thumba la Benjamini n’kuwauza kuti aba kapuyo. Antchito a Yosefe anapeza kapuyo m’thumba la Benjamini ndipo izi zinadabwitsa kwambiri abale akewo. Iwo anapempha Yosefe kuti awalange iwowo m’malo mwa Benjamini.
Apa Yosefe anadziwa kuti abale akewo asintha kwambiri. Iye analephera kudzigwira moti anayamba kulira n’kunena kuti: ‘Ndine Yosefe, m’bale wanu uja. Kodi bambo adakali moyo?’ Abale akewo anadabwa kwambiri. Koma iye anawauza kuti: ‘Musadandaule ndi zimene munandichitira zija. Mulungu ndi amene ananditumiza kuno kuti akupulumutseni. Pitani mukatenge bambo mubwere nawo kuno.’
Abale akewo anapita kukauza bambo awo nkhani yabwinoyi ndipo anawatenga n’kupita nawo ku Iguputo. Yosefe ndi bambo akewo atakumananso anasangalala kwambiri chifukwa panali patadutsa zaka zambiri asanaonane.
“Ngati simukhululukira anthu machimo awo, Atate wanu sadzakukhululukirani machimo anu.”—Mateyu 6:15