Mawu Ofotokoza Chigawo 4
Chigawochi chikufotokoza nkhani ya Yosefe, Yobu, Mose komanso Aisiraeli. Onsewa anapirira mayesero osiyanasiyana ochokera kwa Mdyerekezi. Ena mwa anthuwa anachitiridwa zinthu zopanda chilungamo, kuikidwa m’ndende ngakhalenso kuphedwa kumene. Koma Yehova anawateteza m’njira zosiyanasiyana. Ngati ndinu kholo, thandizani mwana wanu kumvetsa mmene atumiki a Yehova amenewa anavutikira koma n’kukhalabe okhulupirika.
Yehova anagwiritsa ntchito Miliri 10 pofuna kusonyeza kuti iyeyo ndi wamphamvu kwambiri kuposa milungu ya Aiguputo. Fotokozani mmene Yehova anatetezera anthu ake m’mbuyomu komanso mmene akuwatetezera masiku ano.
M'CHIGAWO ICHI
MUTU 14
Kapolo Amene Ankamvera Mulungu
Yosefe ankachita zabwino koma anavutika kwambiri. N’chifukwa chiyani?
MUTU 15
Yehova Sanamuiwale Yosefe
Ngakhale kuti Yosefe anali kutali ndi achibale ake, Yehova anali naye.
MUTU 17
Mose Anasankha Kuti Azilambira Yehova
Mose ali mwana anapulumuka chifukwa cha nzeru za mayi ake.
MUTU 19
Miliri Itatu Yoyambirira
Farao anabweretsera anthu ake mavuto chifukwa anali wonyada ndipo anakana kuti anthu a Mulungu apite.
MUTU 22
Pa Nyanja Yofiira Panachitika Zodabwitsa Kwambiri
Farao sanafe ndi miliri 10. Koma kodi anapulumukanso pa chozizwitsa cha pa Nyanja Yofiirachi?