Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 1

Mulungu Analenga Kumwamba ndi Dziko Lapansi

Mulungu Analenga Kumwamba ndi Dziko Lapansi

Yehova Mulungu ndi amene anatilenga. Komabe sitingathe kumuona. Iye analenganso zinthu zonse zimene timaonazi komanso zimene sitingathe kuziona. Koma asanalenge zinthu zimene timaonazi, analenga angelo ambirimbiri. Kodi umawadziwa angelo? Angelo ndi osiyana ndi anthu, ndipo nawonso sitingathe kuwaona. Mngelo woyamba kulengedwa anathandiza Yehova kulenga zinthu zina zonse. Anamuthandiza kulenga zinthu monga nyenyezi ndi mapulaneti. Limodzi mwa mapulaneti amenewo ndi dziko lathu lapansi lokongolali.

Kenako Yehova anakonza dziko lapansi kuti pazikhala nyama ndi anthu. Anapangitsanso kuti kuwala kwa dzuwa kuzifika padzikoli. Komanso analenga mapiri, nyanja ndi mitsinje.

Kodi ukudziwa zimene anachita kenako? Yehova anati: ‘Ndipanga udzu, mitengo ndi zomera zina.’ Choncho padzikoli panayamba kumera mitengo ya zipatso, maluwa komanso zinthu zina. Kenako analenga nyama zosiyanasiyana, zina zouluka, zina zam’madzi ndipo zina zinali zokwawa. Nyama zina zinali zazing’ono monga akalulu ndipo zina zinali zazikulu monga njovu. Kodi iweyo nyama imene imakusangalatsa ndi iti?

Kenako Yehova anauza mngelo woyamba uja kuti: “Tiyeni tipange munthu.” Anthu analengedwa mosiyana ndi nyama. Amatha kupanga zinthu monga kulankhula, kuseka komanso kupemphera. Yehova anauza anthuwo kuti aziyang’anira dziko lapansi ndi nyama. Kodi ukudziwa kuti munthu woyamba kulengedwa anali ndani? Tiona m’mutu wotsatira.

“Pa chiyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.”​—Genesis 1:1