MUTU 49
Yehova Anapereka Chilango kwa Mfumukazi Yoipa
Mfumu Ahabu akayang’ana pawindo ali m’nyumba yake ku Yezereeli, ankaona munda wa mpesa wa Naboti. Ahabu ankaufuna kwambiri mundawo ndipo anauza Naboti kuti amugulitse. Koma Naboti anakana chifukwa Chilamulo cha Yehova chinkaletsa anthu kugulitsa cholowa kapena kuti zinthu zimene anapatsidwa ndi makolo awo. Kodi Ahabu anasangalala kuti Naboti wachita zoyenera? Ayi. M’malomwake iye anakwiya kwambiri ndipo anakana kudya komanso sanatuluke kuchipinda kwake.
Ndiyeno mkazi wake Yezebeli yemwe anali woipa kwambiri anamuuza kuti: ‘Ndinu mfumu ya Isiraeli. Choncho mungathe kupeza chilichonse chimene mukufuna. Ndipanga zotheka kuti mundawu ukhale wanu.’ Yezebeli analemba makalata kwa akuluakulu a mzinda n’kuwauza kuti amunamizire Naboti kuti wanyoza Mulungu ndipo amuphe pomugenda ndi miyala. Akuluakuluwo anachitadi zimenezi. Kenako Yezebeli anauza Ahabu kuti: ‘Naboti wafa. Tsopano munda uja ndi wanu.’
Koma sikuti Yezebeli anapha Naboti yekha. Iye anaphanso anthu ambiri osalakwa amene ankakonda Yehova. Komanso Yezebeli ankalambira mafano ndiponso ankachita zinthu zambiri zoipa. Yehova ankaona zonsezi. Ndiye kodi anatani?
Ahabu atamwalira, mwana wake Yehoramu, anakhala mfumu. Yehova anatumiza munthu wina dzina lake Yehu kuti akapereke chilango kwa Yezebeli ndi banja lake.
Yehu anakwera galeta n’kuuyamba ulendo wopita ku Yezereeli kumene Yezebeli ankakhala. Atatsala pang’ono kufika, Yehoramu anamuchingamira pa galeta lake. Ndiyeno anamufunsa kuti: ‘Kodi ukubwerera zamtendere Yehu?’ Koma Yehu anayankha kuti: ‘Mtendere ungakhalepo bwanji, mayi ako a Yezebeli akuchita zoipa zambirimbiri?’ Yehoramu
atamva zimenezi anatembenuza galeta lake n’kuyamba kuthawa. Koma Yehu anamubaya ndipo anafera pompo.Kenako Yehu anapita kunyumba kwa Yezebeli. Yezebeli atamva kuti Yehu akubwera, anadzikongoletsa n’kukonzanso tsitsi lake ndipo anapita pawindo n’kumakamudikira. Yehu atafika, Yezebeli anamulonjera mwachipongwe. Ndiyeno Yehu anauza antchito a Yezebeli kuti: “M’ponyeni pansi.” Iwo anaponyadi Yezebeli kudzera pawindo ndipo anagwera pansi n’kufa.
Zitatero Yehu anapha ana aamuna 70 a Ahabu n’kuthetsa kulambira Baala m’dziko lonselo. Kodi waona kuti Yehova amadziwa zonse ndipo pa nthawi yoyenera amapereka chilango kwa anthu amene akuchita zoipa?
“Cholowa chopezedwa mwadyera poyamba, tsogolo lake silidzadalitsidwa.”—Miyambo 20:21