MUTU 92
Yesu Anakumana ndi Asodzi
Patapita nthawi kuchokera pamene Yesu anakumana ndi atumwi, Petulo anaganiza zokapha nsomba kunyanja ya Galileya. Tomasi, Yakobo ndi Yohane nawonso anapita. Iwo anagwira ntchito usiku wonse koma sanaphe kalikonse.
Kutacha, anaona munthu wina ataima m’mbali mwa nyanja. Munthuyo anawafunsa kuti: ‘Koma mwapha nsomba inu?’ Iwo anayankha kuti: ‘Ayi ndithu.’ Ndiyeno anawauza kuti: ‘Ponyani ukonde wanuwo mbali yakumanja.’ Atatero anakola nsomba zambiri moti analephera kuzikokera kumtunda. Nthawi yomweyo, Yohane anazindikira kuti munthuyo ndi Yesu ndipo anati: ‘Aa eti ndi Ambuye!’ Petulo atangomva zimenezi analumphira m’madzi n’kuyamba kusambira kupita kumtunda. Ophunzira enawo anamutsatira pa ngalawa.
Atafika kumtunda, anapeza nsomba ndi mkate zili pamoto. Yesu anawauza kuti amupatseko nsomba zina kuti awonjezere chakudyacho. Kenako anawauza kuti: ‘Bwerani tidye chakudya cham’mawa.’
Atatha kudya, Yesu anafunsa Petulo kuti: ‘Kodi umandikonda kuposa ntchito yausodzi?’ Petulo anayankha kuti: ‘Inde Ambuye. Inunso mukudziwa zimenezo.’ Yesu anati: ‘Dyetsa ana a nkhosa anga.’ Kenako Yesu anafunsanso kuti: ‘Petulo, kodi umandikonda?’ Iye anayankha kuti: ‘Ambuye, inu mukudziwa kuti ndimakukondani.’ Yesu anati: “Weta ana a nkhosa anga.” Ndiyeno anamufunsanso kachitatu ndipo Petulo anamva chisoni n’kuyankha kuti: ‘Ambuye, inu mumadziwa zonse. Mukudziwa kuti ndimakukondani.’ Yesu ananenanso kuti: ‘Dyetsa ana a nkhosa anga.’ Kenako anamuuzanso kuti: “Pitiriza kunditsatira.”
“[Yesu] anawauza kuti: ‘Nditsatireni, ndipo ndikusandutsani asodzi a anthu.’ Nthawi yomweyo iwo anasiya maukonde awo n’kumutsatira.”—Mateyu 4:19, 20