Mawu Ofotokoza Chigawo 7
Chigawochi chikufotokoza mbiri ya moyo wa Mfumu Sauli komanso Mfumu Davide. Mbiriyi inachitika pafupifupi kwa zaka 80. Poyamba Sauli anali wodzichepetsa komanso ankamvera Mulungu. Koma kenako anasintha n’kusiya kutsatira malangizo a Yehova. Zitatero Yehova anamukana ndipo patapita nthawi anauza Samueli kuti adzoze Davide kuti akhale mfumu. Sauli ankachitira nsanje Davide ndipo mobwerezabwereza anayesa kuti amuphe koma Davideyo sanabwezere. Mwana wa Sauli dzina lake Yonatani, ankadziwa kuti Davide wasankhidwa ndi Yehova choncho anakhala wokhulupirika kwa Davideyo. Davide anachita machimo ena akuluakulu koma nthawi zonse
ankamvera Yehova akamudzudzula. Ngati ndinu kholo, thandizani mwana wanu kuti aziona kufunika kotsatira malangizo a Mulungu nthawi zonse.M'CHIGAWO ICHI
MUTU 39
Mfumu Yoyamba ya Aisiraeli
Mulungu anapatsa Aisiraeli oweruza oti aziwatsogolera koma iwo anapempha kuti akhale ndi mfumu. Samueli anadzoza Sauli kuti akhale mfumu yoyamba koma kenako Yehova anakana Sauliyo. Kodi mukudziwa chifukwa chake?
MUTU 40
Davide Anapha Goliyati
Yehova anasankha Davide kuti adzakhale mfumu yotsatira ya Aisiraeli, ndipo zimene Davide anachita zinasonyeza kuti Yehova anasankha bwino.
MUTU 42
Yonatani Anali Wolimba Mtima Komanso Wokhulupirika
Mwana wa mfumu anakhala mnzake wapamtima wa Davide.