Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 67

Mpanda wa Yerusalemu Unamangidwanso

Mpanda wa Yerusalemu Unamangidwanso

Zimene tafotokoza m’mutu wapitawu zisanachitike, panachitikanso zinthu zina. Nehemiya anali Mwisiraeli ndipo ankagwira ntchito kwa Mfumu Aritasasita ku Susani. Ndiyeno mchimwene wake anafika kuchokera ku Yuda n’kumuuza kuti: ‘Anthu amene anabwerera ku Yerusalemu ali pa mavuto. Mpanda wa mzinda umene Ababulo anauwononga sunakonzedwe.’ Izi zinakhumudwitsa kwambiri Nehemiya. Iye anaganiza zopita ku Yerusalemu kukathandiza anthuwo. Choncho anapemphera kuti mfumu imulole kupita.

Kenako mfumu inazindikira kuti Nehemiya sakusangalala. Ndiyeno inamufunsa kuti: ‘Iwetu suoneka chonchi. Watani?’ Nehemiya anayankha kuti: ‘Ndiyenera kuonekadi wokhumudwa chifukwa mzinda wathu wa Yerusalemu suli bwino.’ Mfumuyo inafunsa kuti: ‘Ndiye ndikuthandize bwanji?’ Nthawi yomweyo Nehemiya anapemphera chamumtima. Kenako anati: ‘Mungandilole kuti ndipite kukamanga mpanda wake?’ Mfumuyo inamulola ndipo inaonetsetsa kuti akhale wotetezeka pa ulendo wake wonsewo. Inalamulanso kuti iye akhale bwanamkubwa wa Yuda ndipo anamupatsa matabwa oti akakonzere zitseko zapageti.

Nehemiya atafika ku Yerusalemu anayendera mpanda wonse. Kenako anasonkhanitsa ansembe ndi atsogoleri n’kuwauza kuti: ‘Akuluakulu, zinthu sizili bwino. Tiyenera kumanganso mpandawu.’ Anthuwo anavomera ndipo ntchito inayambika.

Koma adani a Aisiraeli ankawaseka n’kumati: ‘Nkhandwetu ikhoza kugwetsa kampanda kanuko.’ Koma Aisiraeliwo sanasamale zimenezi ndipo anapitiriza kugwira ntchitoyo. Ankamanga bwinobwino mpandawo ndipo unkaoneka wolimba.

Adaniwo anaganiza zoukira Yerusalemu kuchokera m’mbali zosiyanasiyana. Ayuda atamva zimenezo anachita mantha. Koma Nehemiya anawauza kuti: ‘Musaope. Yehova atithandiza.’ Ndiyeno anaika alonda oti aziteteza anthu ogwira ntchitowo, moti adaniwo sanawaukire.

 Patangotha masiku 52 ntchito yonse yomanga mpanda komanso kukonza mageti inatha. Ndiyeno Nehemiya anaitanitsa Alevi onse ku Yerusalemu kuti adzautsegulire. Anakonza zoti pakhale magulu awiri oimba. Maguluwa anadutsa pamalo okwera a mpandawo pamasitepe a Chipata cha Kumadzi. Ezara ndi gulu lina anapita mbali ina ya mzindawo, ndipo Nehemiya ndi gulu lina anapita mbali ina. Ankatamanda Yehova poimba malipenga, zinganga ndi azeze. Magulu awiriwa anakumana pamalo amene panali kachisi. Kenako anthu onse, amuna, akazi ndi ana omwe, anapereka nsembe kwa Yehova ndipo anachita chikondwerero. Panali phokoso lachisangalalo.

“Chida chilichonse chimene chidzapangidwe kuti chikuvulaze sichidzapambana.”​—Yesaya 54:17