Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 31

Yoswa ndi Anthu a ku Gibeoni

Yoswa ndi Anthu a ku Gibeoni

Anthu ena a ku Kanani anamva zimene zinachitika ku Yeriko. Ndiyeno mafumu angapo anapangana kuti amenyane ndi Aisiraeli. Koma anthu a ku Gibeoni anaganiza njira ina. Anapita kwa Yoswa atavala zovala zong’ambika n’kunena kuti: “Tachokera kudziko lakutali kwambiri.” Tamva za Yehova komanso zimene anakuchitirani ku Iguputo ndi ku Mowabu. Lonjezani kuti simudzamenyana nafe ndipo ife tikhala akapolo anu.’

Yoswa anakhulupirira zimene ananenazi ndipo analonjeza kuti sadzamenyana nawo. Patangodutsa masiku atatu, anazindikira kuti anthuwo sanali akutali. Anali a m’dziko la Kanani lomwelo. Ndiyeno Yoswa anafunsa anthuwo kuti: ‘N’chifukwa chiyani munatinamiza?’ Iwo anayankha kuti: ‘Timaopa. Tikudziwa kuti Yehova Mulungu wanu ndi amene akukumenyerani nkhondo. Chonde musatiphe.’ Yoswa anasunga lonjezo lake ndipo sanawaphe.

Pasanapite nthawi yaitali, mafumu 5 a ku Kanani anakonza zoti amenyane ndi anthu a ku Gibeoni. Ndiyeno Yoswa ndi asilikali ake anayenda usiku wonse kupita kukawalanditsa. Nkhondo inayamba m’mawa ndipo  Akananiwo anayamba kuthawa n’kubalalikira mbali zonse. Ndiyeno kulikonse kumene ankathawirako Yehova ankawagwetsera zimatalala zikuluzikulu. Kenako Yoswa anapempha Yehova kuti aimitse dzuwa. N’chifukwa chiyani iye anapempha zimenezi chikhalirecho dzuwa linali lisanaimepo? N’chifukwa choti ankakhulupirira kwambiri Yehova. Yehova anayankha ndipo dzuwa silinalowe kwa tsiku lathunthu mpaka pamene Aisiraeli anagonjetsa mafumu onsewo ndi asilikali awo.

“Mukati Inde akhaledi Inde, ndipo mukati Ayi akhaledi Ayi, pakuti mawu owonjezera pamenepa achokera kwa woipayo.”​—Mateyu 5:37