MUTU 42
Yonatani Anali Wolimba Mtima Komanso Wokhulupirika
Mwana wamkulu wa Mfumu Sauli anali Yonatani ndipo anali msilikali wolimba mtima. Davide ananena kuti Yonatani ankathamanga kuposa chiwombankhanga ndipo anali wamphamvu kuposa mkango. Tsiku lina, Yonatani anaona asilikali 20 a Afilisiti ali paphiri. Iye anauza mtumiki wake amene ankamunyamulira zida kuti: ‘Awotu tikhoza kuwagonjetsa. Tiye tione ngati Yehova angatipatse chizindikiro. Akatiuza kuti tipite ndiye kuti ndi nthawi yabwino ndipo tikawagonjetsa.’ Nthawi yomweyo Afilisitiwo anafuula kuti: ‘Tabwerani timenyane!’ Yonatani ndi mtumiki wakeyo anakweradi phirilo ndipo anakawagonjetsa.
Popeza Yonatani anali mwana woyamba, anali woyenera kudzalowa ufumu wa Sauli. Koma iye ankadziwa kuti Yehova anasankha Davide ndipo sankamuchitira nsanje. Yonatani ndi Davide ankagwirizana kwambiri ndipo
analonjezana kuti azitetezana. Yonatani anapatsa Davide chovala, lupanga, uta ndi lamba posonyeza kuti ndi mnzake wapamtima.Pa nthawi ina, Davide akuthawa Sauli, mnzakeyu anapita kukamuuza kuti: ‘Limba mtima ndipo usaope chilichonse. Yehova wakusankha kuti ukhale mfumu. Ngakhale bambo anga akudziwa zimenezi.’ Kodi iweyo ungafune kukhala ndi mnzako wabwino ngati Yonatani?
Yonatani ankaika moyo wake pangozi pofuna kuthandiza Davide. Iye ankadziwa zoti Mfumu Sauli akufuna kupha Davide ndiye anauza bambo akewo kuti: ‘Bambo mukudziwa kuti mukulakwa? Kodi Davide wakuyambani chiyani kuti muzifuna kumupha?’ Koma Sauli anamukwiyira kwambiri Yonatani. Patapita zaka, Sauli ndi Yonatani anafera kunkhondo.
Yonatani atafa, Davide anafufuza mwana wake dzina lake Mefiboseti. Atamupeza anamuuza kuti: ‘Bambo ako tinkagwirizana kwambiri choncho ndikusamalira kwa moyo wako wonse. Uzikhala m’nyumba yanga ndipo tizidyera limodzi.’ Apatu Davide anasonyeza kuti sanaiwale Yonatani.
“Lamulo langa ndi ili, mukondane monga mmene inenso ndakukonderani. Palibe amene ali ndi chikondi chachikulu kuposa cha munthu amene wapereka moyo wake chifukwa cha mabwenzi ake.”—Yohane 15:12, 13