MUTU 79
Yesu Anachita Zozizwitsa Zambiri
Yesu anabwera padzikoli kudzalalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Yehova anamupatsa mzimu woyera kuti azitha kuchita zozizwitsa. Anachita izi pofuna kusonyeza zimene Yesu adzachite akamadzalamulira dziko lapansili. Yesu ankatha kuchiritsa matenda alionse. Akapita kulikonse, anthu ankamupempha kuti awachiritse ndipo ankawachiritsadi. Ankachiritsa osaona, osamva, ofa ziwalo komanso ankachotsa ziwanda. Ngakhale kungogwira zovala zake, munthu ankatha kuchira. Kulikonse kumene Yesu wapita, anthu ankamutsatira. Nthawi zina ankafuna kukhala payekha koma anthu ankamutsatirabe ndipo iye sankawathamangitsa.
Tsiku lina anthu anabwera ndi munthu wofa ziwalo kunyumba imene Yesu anali. Koma sanathe kulowa chifukwa m’nyumbamo munali anthu ambiri. Choncho anthuwo anaboola padenga n’kutsitsira munthuyo m’kati. Yesu ataona munthuyo anamuuza kuti: ‘Imirira uziyenda.’ Munthuyo anayambadi kuyenda ndipo anthu anadabwa kwambiri.
Yesu akulowa m’mudzi wina anthu akhate 10 anaima chapatali n’kukuwa kuti: ‘Yesu tithandizeni!’ Pa nthawiyo munthu wodwala khate sankaloledwa kukhala pafupi ndi anthu. Yesu anauza akhatewo kuti apite kukachisi. Chilamulo cha Yehova chinkati munthu wakhate akachira, azipita kukachisi kukadzionetsa kwa ansembe. Ali m’njira, onse anazindikira kuti achira. Zitatero mmodzi anabwerera n’kupita kukathokoza Yesu ndipo ankatamanda Mulungu. Pa akhate 10 onsewo, ndi mmodzi yekhayu amene anapita kukathokoza.
Panalinso mayi wina amene anadwala kwa zaka 12 ndipo ankafunitsitsa atachira. Choncho ataona Yesu anayamba kumutsatira ndipo kenako anagwira m’mphepete mwa malaya ake akunja. Nthawi yomweyo anachira. Zitatere Yesu anafunsa kuti: “Ndani wandigwira?” Mayiyo anachita mantha, komabe anabwera pafupi n’kumuuza Yesu chilungamo. Yesu anamulimbikitsa pomuuza kuti: ‘Mwanawe, pita mu mtendere.’
Komanso mtsogoleri wina wa sunagoge dzina lake Yairo anapempha Yesu kuti: ‘Tiyeni tipite kunyumba kwanga kuti mukachiritse mwana wanga wamkazi yemwe akudwala kwambiri.’ Koma Yesu asanafike kunyumba kwa Yairo, mwanayo anamwalira. Yesu atafikako, anapeza anthu ambiri amene anabwera kudzakhala ndi banjalo pa nthawi yovutayi. Yesu anawauza kuti: ‘Musalire, mwanayu sanamwalire koma akugona.’ Kenako anagwira dzanja la mwanayo n’kunena kuti: “Mtsikana iwe, dzuka!” Nthawi yomweyo anadzuka n’kukhala tsonga ndipo Yesu anauza makolo ake kuti amupatse chakudya. Ukuganiza kuti makolo akewo anamva bwanji ataona kuti mwana wawo ali moyo?
“Mulungu anamudzoza ndi mzimu woyera ndi mphamvu. Ndiponso kuti popeza Mulungu anali naye, anayendayenda m’dziko, n’kumachita zabwino ndi kuchiritsa onse osautsidwa ndi Mdyerekezi.”—Machitidwe 10:38