Mawu Ofotokoza Chigawo 5
Patangotha miyezi iwiri kuchokera pamene anawoloka Nyanja Yofiira, Aisiraeli anafika paphiri la Sinai. Paphirili, Yehova anachita nawo pangano loti akhale anthu ake apadera. Iye ankawateteza komanso kuwapatsa zofunika pa moyo. Ankawapatsa malo abwino oti azikhala, chakudya chothedwa mana komanso zovala zawo sizinkatha. Ngati ndinu kholo, thandizani mwana wanu kudziwa chifukwa chake Yehova anapatsa Aisiraeli Chilamulo, chihema komanso ansembe. Tsindikani ubwino wochita zimene talonjeza, kukhala odzichepetsa komanso okhulupirika kwa Yehova.
M'CHIGAWO ICHI
MUTU 23
Analonjeza Kuti Azimvera Yehova
Atafika paphiri la Sinai, Aisiraeli analonjeza Mulungu kuti azimumvera.
MUTU 24
Aisiraeli Sanachite Zimene Analonjeza
Mose ali kokatenga Malamulo 10, Aisiraeli anachimwira Mulungu.
MUTU 26
Anthu 12 Anapita Kukaona Dziko la Kanani
Yoswa ndi Kalebe anali osiyana ndi amuna ena 10 omwe anapita kukaona dziko la Kanani.
MUTU 27
Aisiraeli Ena Anaukira Yehova
Kora, Datani, Abiramu, ndi anthu ena 250 analephera kuzindikira mfundo zofunika zokhudza Yehova.