Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 36

Zimene Yefita Analonjeza

Zimene Yefita Analonjeza

Aisiraeli anasiyanso kutumikira Yehova ndipo anayamba kulambira milungu yonyenga. Pamene a Amoni anawaukira n’kuyamba kumenyana nawo, milungu yonyengayi siinawathandize. Aisiraeli anavutika kwa zaka zambiri. Kenako iwo anauza Yehova kuti: ‘Takuchimwirani, chonde tipulumutseni kwa adani athu.’ Atatero, Aisiraeli anachotsa mafano onse ndipo anayambiranso kulambira Yehova. Yehova sankafuna kuti iwo azingovutikabe.

Choncho anthuwo anasankha Yefita kuti awatsogolere pokamenyana ndi a Amoni. Yefita anauza Yehova kuti: ‘Mukakatithandiza n’kupambana nkhondoyi, ndikulonjeza kuti ndidzapereka kwa inu munthu aliyense wa m’nyumba yanga amene adzayambirire kutuluka kudzandichingamira.’ Yehova anayankha pemphero la Yefita ndipo Aisiraeli anapambanadi pa nkhondoyo.

Pamene Yefita ankabwerera kwawo, munthu woyamba kumuchingamira anali mwana wake wamkazi. Iye anali ndi mwana mmodzi yekhayu basi. Mwana wakeyu anamuchingamira akuvina komanso kuimba maseche. Kodi ndiyeno Yefita anatani? Iye anakumbukira zimene analonjeza zija ndipo anati: ‘Mayo ine mwana wanga! Wandikhumudwitsa. Ndinalonjeza kwa Yehova ndipo kuti ndikwaniritse lonjezolo, ndiyenera kukutumiza kuti uzikatumikira kuchihema ku Silo.’ Koma mwana wakeyo anati: ‘Bambo muyenera kuchita zimene munalonjezazo. Ndikungopempha kuti mundilole ndipite kumapiri ndi anzanga kwa miyezi iwiri. Kenako ndidzapita kuchihemako.’ Mwana wa Yefita anatumikira pachihema mokhulupirika kwa moyo wake wonse. Chaka chilichonse anzake ankapita ku Silo kukamuona.

“Amene amakonda kwambiri bambo ake kapena mayi ake kuposa ine sali woyenera ine.”​—Mateyu 10:37