MUTU 22
Pa Nyanja Yofiira Panachitika Zodabwitsa Kwambiri
Farao atamva kuti Aisiraeli apita, anasintha maganizo. Anauza asilikali ake kuti: ‘Tengani magaleta ankhondo, tiwatsatire. Tisawalole kuti apite.’ Choncho Farao ndi asilikali ake anayamba kuthamangira Aisiraeli.
Yehova ankatsogolera anthu ake. Masana ankagwiritsira ntchito mtambo ndipo usiku ankagwiritsa ntchito moto. Aisiraeliwo atafika pa Nyanja Yofiira Yehova anawauza kuti amange misasa.
Kenako Aisiraeli anaona Farao ndi asilikali ake akuwalondola. Analibe kothawira chifukwa kutsogolo kwawo kunali nyanja ndipo kumbuyo n’kumene kunali asilikaliwo. Iwo anachita mantha kwambiri ndipo analirira Mose kuti: ‘Tifa basi! Bola ukanangotisiya ku Iguputo konkuja.’ Koma Mose anawauza kuti: ‘Musaope! Yehova atipulumutsa.’ Apa Mose anasonyeza kuti ankakhulupirira kwambiri Yehova.
Ndiyeno Yehova anauza Aisiraeli kuti anyamuke. Usiku umenewo, Yehova anachititsa kuti mtambo uja ukhale pakati pa Aisiraeliwo ndi Aiguputo. Zimenezi zinachititsa kuti kumbali ya Aiguputo kukhale mdima, pamene kumbali ya Aisiraeli kunkawala.
Yehova anauza Mose kuti atambasule dzanja lake kuloza panyanja. Ndiyeno Yehova anachititsa mphepo yamphamvu kuwomba panyanjapo usiku wonse. Kenako nyanjayo inagawikana ndipo madzi anaima ngati makoma m’mbali zonse. Aisiraeli anawoloka pouma kupita kutsidya la nyanjayo.
Asilikali a Farao anawatsatira kulowa pakati pa makoma amadziwo. Zitatero Yehova anachititsa kuti asilikaliwo asokonezeke. Mateyala a magaleta awo anayamba kuguluka. Ataona zimenezi asilikaliwo anafuula kuti: ‘Tiyeni tithawe! Yehova akuwamenyera nkhondo.’
Kenako Yehova anauza Mose kuti: ‘Tambasula dzanja lako ndi kuloza panyanja.’ Nthawi yomweyo madzi aja anabwerera m’malo mwake n’kumiza asilikali onse a Aiguputo. Farao ndi asilikali ake anafera pomwepo. Palibe ngakhale mmodzi amene anapulumuka.
Aisiraeliwo ataona kuti apulumuka anatamanda Mulungu poimba kuti: “Ndiimbira Yehova, pakuti iye wakwezeka koposa. Waponyera m’nyanja mahatchi ndi okwera pamahatchiwo.” Poimba nyimboyi, azimayi ankavina ndipo ena ankaimba maseche. Aliyense anasangalala kwambiri.
“Tikhale olimba mtima ndithu ndipo tinene kuti: ‘Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa. Munthu angandichite chiyani?’”—Aheberi 13:6