Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 70

Angelo Analengeza za Kubadwa kwa Yesu

Angelo Analengeza za Kubadwa kwa Yesu

Pa nthawi ina mu ulamuliro wa Kaisara Augusito, panaperekedwa lamulo loti Ayuda onse abwerere m’mizinda ya kwawo kuti akalembetse m’kaundula. Yosefe ndi Mariya anapita ku Betelehemu komwe kunali kwawo kwa Yosefe. Apa n’kuti Mariya atatsala pang’ono kubereka.

Atafika ku Betelehemu, anapeza kuti nyumba zonse ndi zodzaza moti anagona m’khola. Zimenezi zinachititsa kuti Yesu anabadwire m’kholamo. Mariya anakulunga mwanayo ndi nsalu zabwino n’kumugoneka modyetsera ziweto.

Pa nthawiyo, abusa ena ankagona kutchire pafupi ndi ku Betelehemu n’kumayang’anira nkhosa zawo. Mwadzidzidzi, mngelo anafika ndipo pamalo onsewo panawala kusonyeza ulemerero wa Yehova. Abusawo anachita mantha koma mngeloyo anati: ‘Musaope. Ndabwera ndi uthenga wosangalatsa. Lero Mesiya wabadwa ku Betelehemu.’ Nthawi yomweyo, angelo ambirimbiri anaoneka m’mlengalenga ndipo ankanena kuti: ‘Alemekezeke Mulungu kumwamba ndipo mtendere ukhale padziko lapansi.’ Kenako angelowo sanaonekenso. Kodi ukudziwa zimene abusawo anachita?

Anauzana kuti: ‘Tiyeni ku Betelehemu pompanopompano.’ Nthawi yomweyo ananyamuka ndipo atafika anaona Yosefe ndi Mariya ali ndi kamwana kawo m’khola.

Aliyense amene anamva zimene angelowo anauza abusawo anadabwa kwambiri. Mariya anaganizira kwambiri mawu a angelowo ndipo sanawaiwale. Abusawo anabwerera kutchire kuja uku akuthokoza Yehova chifukwa cha zonse zimene anaona.

“Ine ndinachokera kwa Mulungu ndipo ndili pano. Sindinabwere mwakufuna kwanga ayi, koma Iyeyo anandituma.”​—Yohane 8:42