Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 9

Anakhala Ndi Mwana Atakalamba

Anakhala Ndi Mwana Atakalamba

Abulahamu ndi Sara anali atakhala m’banja kwa zaka zambiri. Iwo anasiya nyumba yabwino ku Uri n’kumakhala m’mahema. Koma Sara sankadandaula chifukwa ankakhulupirira Yehova.

Sara ankafunitsitsa atakhala ndi mwana, moti anauza Abulahamu kuti: ‘Hagara, wantchito wangayu atakhala ndi mwana ndingamam’tenge ngati wanga.’ Patapita nthawi, Hagara anakhaladi ndi mwana wamwamuna. Dzina lake anali Isimaeli.

Patadutsa zaka zambiri, kunyumba kwa Abulahamu ndi Sara kunafika alendo atatu. Pa nthawiyi n’kuti Abulahamu ali ndi zaka 99 ndipo Sara anali ndi zaka 89. Abulahamu anaitanira alendowo pansi pa mtengo kuti apume ndipo anawakonzera chakudya. Kodi ukudziwa kuti alendowo anali ndani? Anali angelo. Alendowo anauza Abulahamu kuti: ‘Chaka chamawa nthawi ngati yomwe ino, iwe ndi mkazi wako mudzakhala ndi mwana wamwamuna.’ Sara ankamva zimenezi ali muhema ndipo anayamba kuseka. Iye ankaganiza kuti: ‘Koma zoona mmene ndakalambiramu ndingakhaledi ndi mwana?’

Koma chaka chotsatira, zimene mngelo wa Yehova uja ananena zinachitikadi. Sara anabereka mwana wamwamuna. Ndiyeno Abulahamu anamupatsa dzina loti Isaki, kutanthauza “Kuseka.”

Isaki ali ndi zaka 5, Sara anaona Isimaeli akumuseka Isakiyo. Pofuna kuteteza mwana wakeyo, anauza Abulahamu kuti athamangitse Hagara ndi Isimaeli. Poyamba, Abulahamu sankafuna kuchita zimenezi. Koma Yehova anamuuza kuti: ‘Mvera zimene Sara akunena. Ndidzasamalira Isimaeli. Koma zimene ndinakulonjeza zija zidzakwaniritsidwa kudzera mwa Isaki.’

“Mwa chikhulupiriro, Sara nayenso analandira mphamvu yokhala ndi pakati . . . chifukwa anaona kuti wolonjezayo ndi wokhulupirika.”​—Aheberi 11:11