MUTU 69
Gabirieli Anaonekera kwa Mariya
Elizabeti anali ndi m’bale wake wachitsikana dzina lake Mariya. Iye ankakhala mumzinda wa Nazarete ku Galileya. Mtsikanayu anali pa chibwenzi ndi kalipentala wina dzina lake Yosefe. Ndiyeno patatha miyezi 6 Elizabeti ali woyembekezera, mngelo Gabirieli anapita kwa Mariya n’kumuuza kuti: ‘Mtendere ukhale nawe Mariya. Yehova wakulemekeza kwambiri.’ Mariya sanamvetse zimene mngeloyu ankatanthauza. Ndiyeno Gabirieli anamuuza kuti: ‘Udzakhala ndi mwana wamwamuna ndipo udzamupatse dzina loti Yesu. Iye adzakhala Mfumu ndipo Ufumu wake sudzatha.’
Mariya anati: ‘Kodi zimenezi zingatheke bwanji? Inetu sindinagonepo ndi mwamuna.’ Gabirieli anamuuza kuti: ‘Mulungu sangalephere kuchita chilichonse. Mzimu woyera udzakuthandiza kuti ukhale ndi mwana. Kodi ukudziwa kuti panopa Elizabeti ndi woyembekezera?’ Zitatero, Mariya anayankha kuti: ‘Ndine kapolo wa Yehova. Zimene mwanenazo zichitike ndithu kwa ine.’
Mariya anauyamba ulendo wopita kukaona Elizabeti. Pa nthawiyi, Elizabeti ankakhala mumzinda winawake wakumapiri. Atafika, n’kupereka moni, mwana amene anali m’mimba mwa Elizabeti anayamba kudumpha. Ndiyeno Elizabeti anadzazidwa ndi mzimu woyera n’kuyamba kunena kuti: ‘Mariya, Yehova wakudalitsa. Ndi mwayi waukulu kuti mayi wa Ambuye wanga wafika m’nyumba mwanga.’ Mariya anati: ‘Ndikutamanda Yehova ndi mtima wanga wonse.’ Mariya anakhala ndi Elizabeti kwa miyezi itatu ndipo kenako anabwerera kwawo ku Nazareti.
Yosefe atamva zoti Mariya ndi woyembekezera ankafuna kuthetsa chibwenzi. Koma ali m’tulo mngelo anamuuza kuti: ‘Usaope kutenga Mariya kuti akhale mkazi wako. Sanachite choipa chilichonse.’ Choncho Yosefe anatengadi Mariya n’kumakakhala naye kwawo.
‘Chilichonse chimene Yehova anafuna kuchita anachita. Anachita zimenezi kumwamba ndi padziko lapansi.’—Salimo 135:6