MUTU 85
Yesu Anachiritsa Munthu pa Tsiku la Sabata
Afarisi ankadana ndi Yesu ndipo ankafuna kuti am’pezere chifukwa kuti amumange. Iwo ankati Yesu sankayenera kumachiritsa anthu pa Sabata. Pa tsiku lina la Sabata, Yesu anakumana ndi munthu wosaona amene ankapemphapempha mumsewu. Iye anauza ophunzira ake kuti: ‘Dikirani muone mmene mphamvu za Mulungu zingamuthandizire munthuyu.’ Kenako Yesu analavulira pansi n’kukanda thope ndi malovuwo. Ndiyeno anapaka thopelo m’maso mwa munthuyo n’kumuuza kuti: “Pita ukasambe m’dziwe la Siloamu.” Munthuyo anapitadi ndipo anayamba kuona.
Anthu anadabwa kwambiri ndi zimenezi moti anati: ‘Kodi munthuyu ndi amene amapemphapempha uja, kapena ndi wina angofanana?’ Munthuyo anati: ‘Ndine ndemwe ndithu ndipo ndinabadwa wosaona.’ Anthuwo anamufunsa kuti: ‘Ndiye zatani kuti uyambe kuona?’ Atawafotokozera zomwe zinachitika, anamutenga n’kupita naye kwa Afarisi.
Munthuyo anauza Afarisiwo kuti: ‘Yesu anakanda thope n’kundipaka m’maso ndipo kenako anandiuza kuti ndikasambe. Ndinapitadi ndipo nditasamba ndinayamba kuona.’ Koma Afarisiwo anati: ‘Ngati Yesu akumachiritsa anthu pa Sabata ndiye kuti mphamvu zake si zochokera kwa Mulungu.’ Koma ena anati: ‘Zikanakhala kuti mphamvu zake si zochokera kwa Mulungu, si bwenzi akuchiritsa anthu.’
Afarisi anaitana makolo ake a munthuyo n’kuwafunsa kuti: ‘Zatheka bwanji kuti mwana wanu
ayambe kuona?’ Koma makolowo anaopa chifukwa Afarisi ankachotsa musunagoge aliyense wokhulupirira Yesu. Choncho anangoyankha kuti: ‘Sitikudziwa. Mufunseni mwiniwakeyo.’ Afarisiwo anafunsa munthuyo mafunso ambirimbiri mpaka iye anawayankha kuti: ‘Ndakuuzani kale zonse. N’chifukwa chiyani mukungondifunsabe?’ Afarisiwo anakwiya ndi zimenezi ndipo anamuponyera kunja.Yesu anapita kumene kunali munthuyo ndipo anamufunsa kuti: ‘Kodi umakhulupirira Mesiya?’ Munthuyo anayankha kuti: ‘Eya ndingamukhulupirire nditakhala kuti ndikumudziwa.’ Yesu anamuuza kuti: ‘Ineyo ndine Mesiya.’ Pamenepatu Yesu anasonyeza kuti anali wokoma mtima. Tikutero chifukwa anachiritsa munthuyo komanso anamuthandiza kuti akhale ndi chikhupiriro.
“Mukulakwitsa chifukwa simudziwa Malemba kapena mphamvu ya Mulungu.”—Mateyu 22:29