Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 20

Miliri Inanso 6

Miliri Inanso 6

Mose ndi Aroni anapita kwa Farao kukamuuza uthenga wochokera kwa Mulungu, wakuti: ‘Ngati sulola kuti anthu anga apite, nditumiza m’dzikoli tizilombo touluka toyamwa magazi.’ Ndiyeno tizilomboto tinadzaza m’nyumba za Aiguputo onse, olemera ndi osauka omwe moti tinali mbwee paliponse. Koma ku Goseni kumene Aisiraeli ankakhala kunalibe tizilomboti. Kuyambira ndi mliri wa nambala 4 umenewu, miliriyi inkangokhudza Aiguputo okha. Choncho Farao anachonderera Mose kuti: ‘Ukandipemphere kwa Yehova kuti achotse tizilomboti. Zikatero ndikulolani kuti mupite.’ Koma Yehova atangochotsa tizilomboto, Farao anasintha maganizo. Iye sanaphunzirepo kanthu.

Yehova anati: ‘Farao akapanda kulola kuti anthu anga apite, ziweto zonse za Aiguputo ziyamba kudwala n’kufa.’ Tsiku lotsatira, ziweto za Aiguputo zinayamba kufa. Koma ziweto za Aisiraeli sizinafe. Ngakhale zinali choncho, Farao sanalolebe kuti Aisiraeli azipita.

Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti apitenso kwa Farao ndipo akaponye phulusa m’mwamba. Phulusalo linasanduka fumbi ndipo linadzaza dziko lonse la Iguputo. Fumbilo likagwera pa munthu kapena ziweto, linkayambitsa zilonda zopweteka kwambiri. Komabe Farao sanalole kuti Aisiraeli apite.

Yehova anatuma Mose kuti apitenso kwa Farao n’kukanena kuti: ‘Kodi sukufunabe kuti anthu anga apite? Mawa ndibweretsa chimvula cha matalala.’ Tsiku lotsatira, Yehova anabweretsa mvula ya matalala, mabingu ndi moto. Ku Iguputo kunali kusanagwepo chimvula ngati chimenecho. Chimvulacho chinawononga mitengo komanso mbewu zonse kupatulapo za ku Goseni. Farao anati: ‘Kandipemphere kwa Yehova kuti aletse mvulayi ndipo ndikulolani kuti muzipita.’ Koma matalalawo ndi mvulayo zitangosiya, Farao anasinthanso maganizo.

Kenako Mose anati: ‘Tsopano kugwa dzombe ndipo lidya zomera zonse zimene sizinawonongedwe ndi matalala.’ Choncho kunagwa dzombe lambiri moti linadya mbewu zonse komanso masamba onse a mitengo. Farao anachondereranso kuti: ‘Kandipemphere kwa Yehova kuti achotse dzombeli.’ Koma Yehova atachotsa dzombelo, Farao anakanabe kulola kuti Aisiraeli apite.

Yehova anauza Mose kuti: ‘Tambasula dzanja lako ndipo uloze kumwamba.’ Nthawi yomweyo, kunachita mdima wandiweyani. Kwa masiku atatu, Aiguputo sankatha kuona munthu aliyense kapena chinthu chilichonse. Koma m’nyumba za Aisiraeli munkawala.

Zitatero Farao anauza Mose kuti: ‘Zipitani, koma ziweto zanu muzisiye.’ Koma Mose anati: ‘Tizitenga chifukwa tikufuna kukapereka nsembe kwa Mulungu wathu.’ Farao anakwiya kwambiri n’kunena kuti: ‘Choka! Ndisadzakuonenso. Ndipo ukadzangobweranso ndidzakupha.’

“Anthu inu mudzaonanso kusiyana pakati pa munthu wolungama ndi woipa ndiponso pakati pa munthu amene akutumikira Mulungu ndi amene sanatumikirepo Mulungu.”—Malaki 3:18