MUTU 33
Rute ndi Naomi
Pa nthawi ina, ku Isiraeli kunali njala. Ndiyeno Naomi ananyamuka ndi mwamuna wake komanso ana ake aamuna awiri kupita ku Mowabu. Ali kumeneko mwamuna wa Naomi anamwalira. Ana ake aja anakwatira akazi achimowabu ndipo akaziwo anali Rute ndi Olipa. Koma patapita nthawi, ana onse aamunawo anamwaliranso.
Naomi anamva kuti njala ku Isiraeli yatha ndipo anaganiza zobwerera kwawo. Rute ndi Olipa ananyamuka nawo limodzi koma ali panjira, Naomi anawauza kuti: ‘Ndinu akazi abwino kwambiri. Munkathandiza ana anga komanso ineyo. Koma bwererani kwanu ku Mowabu ndipo mukhoza kukakwatiwanso.’ Rute ndi Olipa anati: ‘Timakukondani kwambiri ndipo sitikufuna kuti tisiyane.’ Naomi anawaumiriza kuti abwerere. Pamapeto pake, Olipa anabwerera koma Rute sanabwerere. Naomi anauza Rute kuti: ‘Iwe, taona Olipa akubwerera kwa anthu ake ndi milungu yake. Bwerera naye limodzi, pita kunyumba kwa mayi ako.’ Koma Rute anati: ‘Sindingakusiyeni. Anthu anu adzakhala anthu anga ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga.’ Kodi ukuganiza kuti Naomi anamva bwanji Rute atanena zimenezi?
Naomi ndi Rute anafika ku Isiraeli nthawi yokolola balere itangoyamba. Tsiku lina Rute anapita kukakunkha balere wotsalira m’munda mwa bambo wina dzina lake Boazi. Bamboyu anali mwana wa Rahabi. Atamva zoti Rute anali wa ku Mowabu koma ankakhalabe ndi Naomi, anauza antchito ake kuti azimusiyira barele wina kuti atenge.
Tsiku lina Rute atabwerera madzulo, Naomi anamufunsa kuti: ‘Kodi lero unakakunkha kuti balere?’ Rute anayankha kuti: ‘M’munda mwa bambo enaake dzina lawo a Boazi.’ Ndiyeno Naomi anati: ‘Amenewotu ndi achibale a mwamuna wanga. Nthawi zonse uzipita m’munda wawo limodzi ndi atsikana ena. Sangakuchite chipongwe.’
Rute ankapitadi kumunda wa Boazi mpaka pamene nyengo yokolola inatha. Boazi anaona kuti Rute ankagwira ntchito mwakhama ndipo anali mkazi wabwino kwambiri. Kalelo munthu akamwalira wopanda mwana, wachibale wake ankakwatira mkazi wamasiyeyo. Choncho Boazi anakwatira Rute. Iwo anabereka mwana dzina lake Obedi. Anzake a Naomi anasangalala kwambiri. Iwo ankanena kuti: ‘Yehova anakupatsa Rute ndipo wakhala akukuthandiza kwambiri. Tsopano wakupatsa chidzukulu. Yehova atamandike.’ Obedi anadzakhala agogo ake a Mfumu Davide.
“Pali bwenzi limene limamatirira kuposa m’bale wako.”—Miyambo 18:24