MUTU 56
Yosiya Ankakonda Chilamulo cha Mulungu
Yosiya anayamba kulamulira ku Yuda ali ndi zaka 8. Pa nthawiyo, anthu ambiri ankakonda zamatsenga ndipo ankalambira mafano. Yosiya atakwanitsa zaka 16 anayesetsa kuphunzira za Yehova kuti azimulambira moyenera. Atakwanitsa zaka 20 anayamba kuphwanya mafano ndi kugumula malo onse amene anthu ankaperekerapo nsembe za mafanowo. Ndiyeno atakwanitsa zaka 26 anakonza zoti kachisi akonzedwe.
Pokonza kachisiyo, mkulu wa ansembe dzina lake Hilikiya anapeza mpukutu wa Chilamulo cha Yehova. N’kutheka kuti umenewu unali mpukutu weniweni umene Mose analemba. Ndiyeno mlembi wa mfumu, dzina lake Safani, anatenga mpukutuwo kupita nawo kwa Yosiya n’kuyamba kumuwerengera mokweza. Yosiya atamva zimene zinali mumpukutuwo, anazindikira kuti anthu akhala asakumvera Yehova kwa zaka zambiri. Kenako anauza Hilikiya kuti: ‘Yehova watikwiyira kwambiri. Pitani mukalankhule naye kuti atiuze zoyenera kuchita.’ Yehova anayankha pogwiritsa ntchito mneneri wamkazi dzina lake Hulida ndipo anati: ‘Ayuda asiya kutsatira malamulo anga. Ndiwalanga ndithu. Koma sindichita zimenezi pa nthawi ya Yosiya chifukwa wadzichepetsa.’
Yosiya atamva zimenezi anapita kukachisi n’kuitanitsa Ayuda onse ndipo anawawerengera Chilamulo cha Yehova. Onse analonjeza kuti ayamba kumvera Yehova ndi mtima wonse.
Ayudawo anali atasiya kuchita Pasika kwa zaka zambiri. Koma Yosiya anamva m’Chilamulocho kuti iwo ayenera kuchita Pasika chaka chilichonse.
Choncho anauza Ayudawo kuti: ‘Tiyeni tichitire Yehova Pasika.’ Yosiyayo anakonza zoti paperekedwe nsembe zambiri komanso kuti pakhale anthu oimba pakachisi. Ayudawo anachita Pasika ndipo kenako anachita Chikondwerero cha Mikate Yopanda Chofufumitsa kwa masiku 7. Panali pasanachitike Pasika ngati ameneyu chimwalirire Samueli. Izi zikusonyeza kuti Yosiya ankakonda kwambiri Chilamulo cha Yehova. Kodi iweyo umasangalala kuphunzira za Yehova?“Mawu anu ndi nyale younikira kumapazi anga, ndi kuwala kounikira njira yanga.”—Salimo 119:105