Mawu Ofotokoza Chigawo cha 12
Yesu anaphunzitsa anthu zokhudza Ufumu wakumwamba. Iye anawaphunzitsanso kuti azipemphera kuti dzina la Mulungu liyeretsedwe, Ufumu wake ubwere komanso chifuniro chake chichitike padzikoli. Ngati ndinu kholo, fotokozerani mwana wanuyo chifukwa chake pempheroli ndi lofunika kwa ife. Yesu sanalole kuti Satana amulepheretse kukhala wokhulupirika kwa Mulungu. Iye anasankha atumwi ake ndipo iwo ndi amene anali oyamba kusankhidwa kuti adzalamulire nawo mu Ufumu. Ngati ndinu kholo, thandizani mwana wanuyo kuti aone zoti Yesu anali wodzipereka kwambiri pa kulambira koona. Popeza Yesu ankafuna kuthandiza anthu anachiritsa odwala, anadyetsa anjala komanso anaukitsa akufa. Zinthu zodabwitsa zimene anachitazi zinasonyeza zimene Ufumu wa Mulungu udzachitire anthu.
M'CHIGAWO ICHI
MUTU 74
Yesu Anakhala Mesiya
Kodi Yohane ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti Yesu ndi Mwanawankhosa wa Mulungu?
MUTU 75
Mdyerekezi Anayesa Yesu
Mdyerekezi anayesa Yesu katatu. Kodi mayesero ake anali otani? Kodi Yesu anatani?
MUTU 76
Yesu Anayeretsa Kachisi
N’chifukwa chiyani Yesu anatulutsa nyama m’kachisi ndiponso anagubuduza matebulo a osintha ndalama?
MUTU 77
Yesu Anakumana ndi Mayi Pachitsime
N’chifukwa chiyani mayi wachisamariya anadabwa kuona kuti Yesu akumulankhula? Kodi Yesu anamuuza mfundo iti yomwe anali asanauze aliyense?
MUTU 78
Yesu Ankalalikira Uthenga wa Ufumu
Yesu anauza ophunzira ake kuti akhala “asodzi a anthu.” Kenako anaphunzitsa ophunzira ake 70 kuti azikalalikira uthenga wabwino.
MUTU 79
Yesu Anachita Zozizwitsa Zambiri
Kulikonse kumene Yesu ankapita, kunkakhala anthu odwala oti awathandize ndipo iye ankawachiritsa. Ndiponso anaukitsa kamtsikana kena.
MUTU 83
Yesu Anadyetsa Anthu Ambiri
Kodi chozizwitsa chimenechi chikutiuza chiyani za Yehova ndi Yesu?
MUTU 84
Yesu Anayenda Panyanja
Kodi mukuganiza kuti atumwi anamva bwanji ataona chozizwitsa chimenechi?
MUTU 85
Yesu Anachiritsa Munthu pa Tsiku la Sabata
N’chifukwa chiyani anthu ena sanasangalale ndi zimene Yesu anachita?
MUTU 86
Yesu Anaukitsa Lazaro
Yesu ataona Mariya akulira, nayenso analira. Koma kenako chisoni chawo chinasanduka chisangalalo.