Mawu Ofotokoza Chigawo 6
Aisiraeli atafika m’Dziko Lolonjezedwa ankalambira Mulungu kuchihema. Ansembe ankaphunzitsa Chilamulo ndipo oweruza ndi amene ankatsogolera anthu. Chigawochi chikufotokoza mmene zosankha komanso zochita za munthu zimakhudzira anthu ena. Munthu aliyense ankafunikira kukonda Yehova komanso anthu ena. Fotokozani mmene zochita za Debora, Naomi, Yoswa, Hana, mwana wamkazi wa Yefita komanso Samueli zinathandizira anthu ena. Tsindikani mfundo yakuti ngakhale anthu a mitundu ina anasankha kugwirizana ndi Aisiraeli chifukwa ankadziwa kuti Mulungu ankawatsogolera. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi Rahabi, Rute, Yaeli ndiponso anthu a ku Gibeoni.
M'CHIGAWO ICHI
MUTU 29
Yehova Anasankha Yoswa
Malangizo amene Mulungu anapereka kwa Yoswa angatithandizenso ifeyo masiku ano.
MUTU 30
Rahabi Anabisa Aisiraeli Okaona Dziko
Mpanda wa mzinda wa Yeriko unagwa. Koma nyumba ya Rahabi sinagwe ngakhale kuti inali yogundizana ndi mpandawo.
MUTU 31
Yoswa ndi Anthu a ku Gibeoni
Yoswa anapemphera kwa Mulungu kuti dzuwa liime. Kodi Mulungu anamumvera?
MUTU 32
Mtsogoleri Watsopano ndi Azimayi Awiri Olimba Mtima
Yoswa atamwalira, Aisiraeli anayamba kulambira mafano. Zinthu zinayamba kusayenda bwino, koma zinthu zinasintha ndi kubwera kwa Woweruza Baraki, Debora mneneri wamkazi komanso Yaeli
MUTU 33
Rute ndi Naomi
Azimayi awiri amene amuna awo anamwalira akubwerera ku Isiraeli. Mmodzi mwa azimayiwo dzina lake Rute anayamba kumakunkha m’minda ya anthu ndipo Boazi anamuona kuti anali wolimbikira ntchito.
MUTU 34
Gidiyoni Anagonjetsa Amidiyani
Amidiyani atayamba kuzunza Aisiraeli, Aisiraeliwo anapempha Yehova kuti awathandize. Kodi zinatheka bwanji kuti asilikali ochepa a Gideoni agonjetse gulu la asilikali okwana 135,000?
MUTU 35
Hana Anapempha Kuti Mulungu Amupatse Mwana Wamwamuna
Elikana anatenga Hana komanso Penina ndi ana ake n’kupita nawo kuchihema ku Silo. Kumeneko Hana anapempha Mulungu kuti amupatse mwana wamwamuna. Patatha chaka anabereka Samueli.
MUTU 36
Zimene Yefita Analonjeza
Kodi Yefita analonjeza chiyani? N’chifukwa chiyani analonjeza? Kodi mwana wake anachita chiyani atamva lonjezolo?
MUTU 37
Yehova Analankhula ndi Samueli
Eli anali Mkulu wa Ansembe ndipo ana ake awiri analinso ansembe. Ana akewa sankamvera malamulo a Mulungu. Koma Samueli ankachita zabwino ndipo tsiku lina Yehova analankhula naye.
MUTU 38
Yehova Anapatsa Mphamvu Samisoni
Yehova anapatsa Samisoni mphamvu kuti agonjetse Afilisiti koma iye atalakwitsa zinthu zina Afilisitiwo anamugwira.