Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 97

Koneliyo Analandira Mzimu Woyera

Koneliyo Analandira Mzimu Woyera

Ku Kaisareya kunali munthu wina dzina lake Koneliyo ndipo anali mkulu wa asilikali. Ngakhale kuti iye sanali Myuda, Ayuda ankamupatsa ulemu. Koneliyo ankathandiza kwambiri anthu ovutika. Iye ankakhulupirira Yehova ndipo ankakonda kupemphera. Tsiku lina kunabwera mngelo ndipo anamuuza kuti: ‘Mulungu wamva mapemphero ako. Tumiza anthu ku Yopa kuti akaitane munthu wina dzina lake Petulo.’ Nthawi yomweyo Koneliyo anatumizadi anthu ku Yopa ndipo unali ulendo wamakilomita 48 kum’mwera kwa Kaisareya.

Pa nthawiyi n’kuti Petulo ali ku Yopa ndipo anthu aja ali m’njira, iye anaona masomphenya. Anaona nyama zimene Ayuda sankaloledwa kudya ndipo anamva mawu omuuza kuti adye nyamazo. Petulo anakana ndipo anati: ‘Ine chibadwire changa sindinadyepo nyama zimenezi.’ Koma mawu aja anamvekanso kuti: ‘Usiye kunena kuti nyama zimenezi n’zodetsedwa chifukwa Mulungu waziyeretsa.’ Kenako Petulo anauzidwa kuti: ‘Pali anthu atatu amene akukufuna. Pita nawo limodzi.’ Petulo anapita kukaona anthuwo ndipo atawalonjera, anamuuza kuti: ‘Watitumiza ndi mkulu wa asilikali wina dzina lake Koneliyo. Akuti tidzakutengeni tipite limodzi kunyumba kwake ku Kaisareya.’ Petulo anawalowetsa m’nyumba ndi kuwasamalira monga alendo ake. Mawa lake ananyamuka nawo ulendo wopita ku Kaisareya. Anapitanso ndi abale angapo a ku Yopa.

Kenako anafika ku Kaisareya. Koneliyo ataona Petulo, anamugwadira n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi. Koma Petulo anamuuza kuti: ‘Imirirani, inenso ndine munthu chabe.’ Kenako anamuuza kuti: ‘Inu mukudziwa kuti Ayuda salowa m’nyumba za anthu a mitundu ina. Koma Mulungu wandiuza kuti ndibwere kunyumba kwanu kuno. Tsopano ndiuzeni chimene mumandifunira.’

Koneliyo anauza Petulo kuti: ‘Masiku 4 apitawo, ndikupemphera kwa Mulungu, mngelo anandiuza kuti nditumize anthu adzakuitaneni. Chonde tiphunzitseni mawu a Mulungu.’ Petulo anati: ‘Ndadziwa kuti Mulungu alibe tsankho. Amalandira aliyense amene amafuna kumulambira.’ Petulo anawaphunzitsa zinthu zambiri zokhudza Yesu. Kenako mzimu woyera unafika pa Koneliyo ndi anthu amene anali naye ndipo onsewo anabatizidwa.

“[Mulungu] amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.”​—Machitidwe 10:35