Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 80

Yesu Anasankha Atumwi 12

Yesu Anasankha Atumwi 12

Yesu atalalikira pafupifupi kwa chaka ndi hafu, ankafunika kuchita zinazake zofunika kwambiri. Anafunika kusankha anthu apadera oti azigwira nawo ntchito yolalikira. Anthuwa anafunikanso kuwaphunzitsa kuti adzathe kutsogolera mpingo wachikhristu iye akadzapita kumwamba. Yesu anaona kuti m’pofunika kuti Yehova amutsogolere posankha anthuwo. Choncho anapita kuphiri kwayekhayekha ndipo anapemphera usiku wonse. Kutacha, anaitana ophunzira ake ena ndipo anasankhapo anthu 12 oti akhale atumwi. Kodi ukukumbukira maina awo? Anali Petulo, Andireya, Yakobo, Yohane, Filipo, Batolomeyo, Tomasi, Mateyu, Yakobo mwana wa Alifeyo, Tadeyo, Simoni ndi Yudasi Isikariyoti.

Andireya, Petulo, Filipo, Yakobo

Atumwi 12 amenewa ankayenda ndi Yesu. Kenako atawaphunzitsa, anayamba kumapita okha. Yehova anawapatsa mphamvu ndipo ankatha kutulutsa ziwanda komanso kuchiritsa odwala.

Yohane, Mateyu, Batolomeyo, Tomasi

Yesu ankaona kuti atumwi 12 amenewa ndi mabwenzi ake ndipo ankawakhulupirira. Koma Afarisi ankaganiza kuti atumwiwo anali osaphunzira komanso anthu wamba. Komatu Yesu anawaphunzitsa  kuti azigwira bwino ntchito yawo. Atumwiwo anakhalabe ndi Yesu pa nthawi yovuta. Mwachitsanzo, analipo Yesu atatsala pang’ono kuphedwa komanso ataukitsidwa. Mofanana ndi Yesu ambiri mwa atumwiwa anali ochokera ku Galileya. Ndipo ena anali okwatira.

Yakobo mwana wa Alifeyo, Yudasi Isikariyoti, Tadeyo, Simoni

Koma atumwiwa anali ochimwa ngati ife tomwe ndipo ankalakwitsa zinthu zina. Pena ankalankhula asanaganize ndiponso ankasankha zolakwika. Nthawi zinanso sankaleza mtima komanso ankakangana kuti wamkulu ndani. Komabe atumwiwa anali anthu abwino ndipo ankakonda Yehova. Iwo ndi amene anali anthu oyamba kukhala mumpingo wachikhristu Yesu atapita kumwamba.

“Ndakutchani mabwenzi, chifukwa zonse zimene ndamva kwa Atate wanga ndakudziwitsani.”​—Yohane 15:15