MUTU 48
Mwana wa Mzimayi Wamasiye Anaukitsidwa
Pamene ku Isiraeli kunali chilala, Yehova anauza Eliya kuti: ‘Pita ku Zarefati. Kumeneko mzimayi wina wamasiye azikakupatsa chakudya.’ Eliya atafika mumzindawo, anaona mzimayi wosauka komanso wamasiye akutola nkhuni. Iye anam’pempha kuti amupatseko madzi. Pamene mzimayiyo ankapita kukatenga madziwo, Eliya anamuuzanso kuti: ‘Mundibweretserekonso chakudya pang’ono.’ Koma mzimayiyo anati: ‘Ndilibe chakudya choti ndingakupatseni. Ndangotsala ndi kaufa kochepa ndi timafuta toti ndiphikire chakudya chokwanira ineyo ndi mwana wanga basi.’ Koma Eliya anamuuza kuti: ‘Yehova wanena kuti mukandipatsa, ndiye kuti ufa ndi mafuta anu sizitha mpaka mvula idzagwa.’
Ndiyeno mzimayiyu anapita kukakonza chakudya ndi kumupatsa mneneri wa Yehovayo. Monga mmene Yehova ananenera, mzimayiyu ndi mwana wake anali ndi chakudya pa nthawi yonse yachilalayo. Mtsuko wake wa ufa komanso wa mafuta unkangokhalabe wodzadza.
Kenako panachitika zinthu zomvetsa chisoni. Mwana uja anadwala kwambiri mpaka kumwalira. Ndiyeno mzimayiyo
anapempha Eliya kuti amuthandize. Eliya anatenga mwana wakufayo n’kupita naye kuchipinda cham’mwamba. Anamugoneka pabedi ndipo anapemphera kuti: ‘Chonde Yehova, ukitsani mwanayu.’Zitatero mwana uja anakhalanso ndi moyo ndipo anayamba kupuma. Eliya anauza mzimayiyo kuti: ‘Mwana wanu uja uyu, ali moyo.’ Mzimayiyo anasangalala kwambiri ndipo anauza Eliya kuti: ‘Ndinudi munthu wa Mulungu. Ndikutero chifukwa mumalankhula zimene Yehova wakuuzani.’ Zimene Yehova anachitazi zinali zodabwitsa kwambiri. Tikutero chifukwa pa nthawiyo panalibe munthu amene anaukitsidwapo. Komanso mzimayiyu ndi mwana wakeyo sanali Aisiraeli.
“Onetsetsani makwangwala, iwo safesa mbewu kapena kukolola. Alibe nyumba yosungiramo zinthu kapena nkhokwe, komatu Mulungu amawadyetsa. Kodi inu si ofunika kwambiri kuposa mbalame?”—Luka 12:24