MUTU 64
Danieli Anaponyedwa M’dzenje la Mikango
Pa nthawi ina Dariyo Mmedi anayamba kulamulira ku Babulo. Iye anaona kuti Danieli anali ndi luso lapadera choncho anamusankha kuti akhale nduna komanso kuti aziyang’anira nduna zinzake. Nduna zinazo ndi anthu ena anayamba kumuchitira nsanje ndipo ankafuna kumupezera chifukwa. Iwo ankadziwa kuti Danieli ankakonda kupemphera kwa Yehova katatu tsiku lililonse. Choncho anauza Dariyo kuti: ‘Mfumu, mukhazikitse lamulo loti aliyense azipemphera kwa inuyo basi. Munthu akapanda kumvera lamuloli, aziponyedwa m’dzenje la mikango.’ Zimenezi zinamusangalatsa Dariyo ndipo anakhazikitsadi lamuloli.
Danieli atangomva za lamulo latsopanoli, anapita kunyumba kwake. Ndipo windo lili chitsegulireni, anagwada n’kuyamba kupemphera kwa Yehova. Anthu amene ankamuchitira nsanje aja ataona, analowa n’kumupeza akupemphera. Zitatero anathamangira kwa Dariyo n’kukamuuza kuti: ‘Mfumu, Danieli sakumvera lamulo lanu lija. Akupitirizabe kupemphera kwa Mulungu wake katatu tsiku lililonse.’ Popeza Dariyo ankakonda kwambiri Danieli, sankafuna kuti aphedwe. Choncho kwa tsiku lonse, anayesetsa kuti apeze njira yomupulumutsira. Koma poti sizinkatheka kuti munthu aliyense asinthe lamulo limene mfumu yasainira, Dariyo analamula kuti Danieli aponyedwe m’dzenje la mikango yolusa.
Tsiku limeneli Dariyo sanagone ndipo ankangoganizira za Danieli. Ndiyeno kutacha, anathamangira kudzenje kuja ndipo anafuula kumufunsa Danieli kuti: ‘Kodi Mulungu wako wakupulumutsa?’
Danieli anayankha kuti: ‘Mngelo wa Yehova anatseka pakamwa pa mikango moti sinandivulaze.’ Dariyo atamva zimenezi anasangalala kwambiri. Ndiyeno analamula kuti Danieli atulutsidwe m’dzenje muja. Iye anatuluka wosakandika paliponse. Zitatero mfumu inalamula kuti: ‘Ponyani m’dzenjemu anthu amene amafunira zoipa Danieli.’ Atangowaponya m’dzenjemo, mikango ija inawakhadzulakhadzula.
Ndiyeno Dariyo analamula anthu ake onse kuti: ‘Aliyense azitamanda Mulungu wa Danieli chifukwa wamupulumutsa m’dzenje la mikango.’
Kodi iweyo umapemphera kwa Yehova tsiku lililonse ngati mmene ankachitira Danieli?
“Yehova amadziwa kupulumutsa anthu odzipereka kwa iye akakhala pa mayesero.”—2 Petulo 2:9