MUTU 62
Ufumu Wofanana ndi Mtengo Waukulu
Tsiku lina Nebukadinezara analota maloto oopsa. Ndiyeno anaitana anthu anzeru a mu ufumu wake kuti amuuze tanthauzo lake. Koma palibe amene anakwanitsa kumasulira malotowo. Kenako Nebukadinezara anauza Danieli maloto akewo.
Anamufotokozera kuti: ‘Ndinalota mtengo womwe unakula kwambiri n’kufika kumwamba. Umaoneka padziko lonse ndipo unali ndi masamba okongola komanso zipatso zambiri. Nyama zakutchire zimakhala mum’thunzi wake komanso mbalame zimamanga zisa munthambi zake. Kenako mngelo anabwera kuchokera kumwamba n’kufuula kuti: “Gwetsani mtengowo ndipo dulani nthambi zake. Koma musiye chitsa chake munthaka, ndipo muchikulunge ndi mkombero wachitsulo ndi wamkuwa. Mtima wake usinthidwe kuti usakhale wa munthu koma wa nyama ndipo padutse nthawi zokwanira 7. Anthu onse adziwe kuti Mulungu ndiye Wolamulira ndipo angathe kupereka ulamuliro kwa munthu aliyense amene akufuna.”’
Yehova anathandiza Danieli kuti adziwe zimene malotowa ankatanthauza. Danieli anachita mantha ndi tanthauzo la malotowo. Anauza Nebukadinezara kuti: ‘Mfumu, malotowa akunena za inu. Koma zikanakhala bwino akanakhala kuti akunena za adani anu. Mtengo waukulu umene unadulidwawo ukuimira inuyo. Mudzasiya kukhala mfumu ndipo mudzapita kutchire n’kumakadya msipu ngati nyama yakutchire. Koma popeza mngelo anati chitsa cha mtengowo chisazulidwe, ndiye kuti mudzabwereranso n’kukhala mfumu.’
Patatha chaka, tsiku lina Nebukadinezara ankayenda padenga la nyumba yake n’kumaona zamphamvu zimene anachita mu ufumu wake. Iye anati: ‘Koma ndiye zinthu zikundiyendera bwino. Taonani mmene mzinda wa Baibulo ukukongolera!’ Koma mawu ake adakali m’kamwa, anamva mawu ochokera kumwamba akuti: ‘Nebukadinezara! Ufumu wachoka m’manja mwako.’
Nthawi yomweyo Nebukadinezara anachita misala ndipo anakhala ngati nyama yakutchire. Anachoka kunyumba yake yachifumu n’kumakakhala kutchire ndi nyama. Tsitsi lake linatalika ngati nthenga za chiwombankhanga ndipo zikhadabo zake zinatalika ngati za mbalame.
Patatha zaka 7, Nebukadinezara anachira ndipo Yehova anamuikanso kukhala mfumu ya Babulo. Kenako iye anati: ‘Ndikutamanda Yehova, Mfumu yakumwamba. Panopa ndadziwa kuti iye ndiye Wolamulira. Amatsitsa anthu odzikweza ndipo angathe kupereka ufumu kwa aliyense amene akufuna.’
“Kunyada kumafikitsa munthu ku chiwonongeko, ndipo mtima wodzikuza umachititsa munthu kupunthwa.”—Miyambo 16:18