Yeremiya 21:1-14

21  Yehova anauza Yeremiya mawu,+ pamene Mfumu Zedekiya+ inatumiza Pasuri+ mwana wa Malikiya ndi Zefaniya+ mwana wa Maaseya, wansembe, ndi uthenga wakuti:  “Chonde tifunsire kwa Yehova+ chifukwa Nebukadirezara mfumu ya Babulo akufuna kumenyana nafe nkhondo.+ Mwina Yehova adzatichitira imodzi mwa ntchito zake zamphamvu kuti Nebukadirezarayo atichokere.”+  Pamenepo Yeremiya anawauza kuti: “Mukauze Zedekiya kuti,  ‘Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Anthu inu, ine ndichititsa zida zimene zili m’manja mwanu kukutembenukirani. Zimenezi ndi zida zimene mukugwiritsa ntchito pomenyana ndi mfumu ya Babulo+ ndi Akasidi+ amene azungulira kunja kwa mpanda wanu. Ndipo ndisonkhanitsa zida zanuzo pakati pa mzinda uwu.+  Ndidzamenyana nanu+ ndi mkono wotambasula ndiponso dzanja lamphamvu. Ndidzachita zimenezi nditakwiya, nditapsa mtima, ndiponso ndili ndi ukali waukulu.+  Ndidzapha onse okhala mumzinda uwu, anthu ndi nyama zomwe. Adzafa ndi mliri waukulu.”’+  “‘Yehova wanena kuti: “Kenako Zedekiya mfumu ya Yuda, atumiki ake ndi anthu onse, onse opulumuka ku mliri, lupanga ndi njala yaikulu mumzinda uwu, ndidzawapereka m’manja mwa Nebukadirezara mfumu ya Babulo. Ndidzawapereka m’manja mwa adani awo ndi m’manja mwa amene akufuna moyo wawo. Nebukadirezara adzawapha ndi lupanga+ ndipo sadzawamvera chisoni, kuwakomera mtima kapena kuwachitira chifundo.”’+  “Anthu awa uwauze kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Anthu inu, ndikuika njira ya moyo ndi njira ya imfa pamaso panu.+  Anthu amene adzakhalabe mumzindawu adzafa ndi lupanga, njala yaikulu ndiponso mliri.+ Koma amene adzatuluka ndi kugwidwa ndi Akasidi amene akuzungulirani adzakhala ndi moyo. Iwo adzapulumutsa moyo wawo.”’+ 10  “‘“Mzinda uwu ndaukana* ndipo ukumana ndi tsoka osati zabwino,”+ watero Yehova. “Ndidzaupereka m’manja mwa mfumu ya Babulo+ ndipo idzautentha ndi moto.”+ 11  “‘Anthu inu, imvani zimene Yehova wanena zokhudza banja la mfumu ya Yuda.+ 12  Inu a m’nyumba ya Davide,+ Yehova wanena kuti: “M’mawa uliwonse+ muziweruza mwachilungamo,+ ndipo muzilanditsa munthu kwa anthu achinyengo amene akufuna kumulanda katundu.+ Muzitero kuti mkwiyo wanga usayake ngati moto+ ndi kukutenthani popanda wouzimitsa chifukwa cha kuipa kwa zochita zanu.”’+ 13  “‘Ndakuukira iwe mkazi wokhala m’chigwa,+ iwe mzinda wapathanthwe limene lili pamalo athyathyathya,’ watero Yehova. ‘Koma inu amene mukunena kuti: “Ndani adzabwera kuno kuti atiukire? Ndipo ndani adzalowa m’nyumba zathu?”+ imvani izi, 14  ndidzakuimbani mlandu+ mogwirizana ndi zipatso za ntchito zanu,’+ watero Yehova. ‘Ndidzayatsanso moto m’nkhalango za mzindawu,+ moti udzanyeketsa zinthu zonse zouzungulira.’”+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “ndauikira nkhope yanga motsutsana nawo.”