Yeremiya 30:1-24
30 Mawu amene Yehova anauza Yeremiya ndi awa:
2 “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Lemba m’buku mawu onse amene ndidzalankhula nawe.+
3 Pakuti, “taona! masiku adzafika,” watero Yehova, “pamene ndidzasonkhanitsa Isiraeli ndi Yuda,+ anthu anga amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina,” watero Yehova. “Iwo ndidzawabwezeretsa kudziko limene ndinapatsa makolo awo ndipo adzalitenga kukhalanso lawo.”’”+
4 Awa ndi mawu amene Yehova wauza Isiraeli ndi Yuda.
5 Yehova wanena kuti: “Ife tamva phokoso la anthu amene akunjenjemera. Iwo agwidwa ndi mantha+ ndipo palibe mtendere.
6 Anthu inu, funsani kuti mudziwe ngati mwamuna angabale mwana.+ N’chifukwa chiyani mwamuna aliyense wamphamvu akuoneka atagwira manja m’chiuno ngati mkazi amene akubala mwana? N’chifukwa chiyani nkhope zawo zonse zafooka?+
7 Kalanga ine! Tsiku limeneli ndi lalikulu+ moti palibe lofanana nalo.+ Limeneli ndi tsiku la masautso kwa Yakobo.+ Koma adzapulumuka m’masautso amenewa.”
8 “Pa tsikuli ndidzathyola goli ndi kulichotsa m’khosi lanu. Ndidzadula zingwe zimene akumangani nazo,+ moti alendowo sadzagwiritsanso ntchito Yakobo monga wantchito wawo,” watero Yehova wa makamu.
9 “Inu mudzatumikira Yehova Mulungu wanu ndi Davide mfumu yanu+ imene ndidzakuutsirani.”+
10 “Koma iwe Yakobo mtumiki wanga usachite mantha, iwe Isiraeli usagwidwe ndi mantha,”+ watero Yehova. “Pakuti ine ndikukupulumutsa kuchokera kutali ndipo ndikupulumutsanso ana ako kuchokera kudziko limene anatengedwa kukakhala akapolo.+ Yakobo adzabwerera ndipo adzakhala mosatekeseka komanso mopanda zosokoneza. Sipadzakhala womuopsa.”+
11 “Pakuti ine ndili ndi iwe kuti ndikupulumutse,”+ watero Yehova. “Ndidzawononga anthu a mitundu yonse ya kumene ndinakubalalitsirani,+ koma iwe sindidzakuwononga.+ Ndidzakuwongolera pa mlingo woyenera chifukwa sindidzakusiya osakulanga.”+
12 Yehova wanena kuti: “Sudzachira kuvulala kwako.+ Chilonda chako cha mkwapulo ndi chosachiritsika.+
13 Palibe amene akuchonderera kuti chilonda chako chipole.+ Palibe njira iliyonse yokuchiritsira ndipo palibe mankhwala amene angakuthandize.+
14 Achigololo onse amene anali kukukonda kwambiri akuiwala.+ Iwo sakukufunafunanso. Ndakumenya ndi mkwapulo+ ngati mdani ndipo ndakulanga ngati munthu wankhanza+ chifukwa cha kuchuluka kwa zolakwa zako.+ Machimo ako achuluka kwambiri.+
15 N’chifukwa chiyani ukulira pamene wadzivulaza mwadala?+ Ululu wako ndi wosachiritsika chifukwa zolakwa zako zachuluka ndipo machimo ako ndi ochuluka kwambiri.+ Ine ndakuchitira zimenezi.
16 Choncho, onse okuwononga adzawonongedwa,+ ndipo adani ako onse adzatengedwa kupita ku ukapolo.+ Amene akulanda katundu wako nawonso adzalandidwa katundu wawo. Onse ofunkha zinthu zako nawonso zinthu zawo zidzafunkhidwa.”+
17 “Ndidzakubwezeretsa mwakale ndipo ndidzachiritsa zilonda zako za mkwapulo,”+ watero Yehova. “Iwo anakutcha kuti mkazi wothamangitsidwa ndipo anali kunena kuti:+ ‘Ameneyu ndi Ziyoni ndipo palibe amene akumufunafuna.’”+
18 Yehova wanena kuti: “Ndikusonkhanitsa anthu a m’mahema a Yakobo+ amene anagwidwa ndi kutengedwa kupita kudziko lina ndipo ndidzamvera chisoni malo okhala a Yakobo. Mzinda udzamangidwanso pachiunda chake+ ndipo nsanja yokhalamo idzakhala pamalo ake oyenera.+
19 Kwa iwo kudzamveka mawu oyamikira ndi phokoso la kuseka kwa anthu.+ Ndidzawachulukitsa moti sadzakhala ochepa.+ Ndidzachulukitsa chiwerengero chawo moti sadzakhala kagulu kakang’ono ka anthu.+
20 Ana ake aamuna adzabwerera mwakale ndipo khamu la anthu ake lidzakhazikika pamaso panga.+ Ndidzalanga onse omupondereza.+
21 Munthu wotchuka adzachokera mwa iye+ ndipo pakati pa anthu ake padzatuluka wolamulira.+ Ndidzamulola kundiyandikira ndipo adzabwera kwa ine.”+
“Tsopano uyu ndani amene wapereka mtima wake ngati chikole kuti ayandikire kwa ine?”+ watero Yehova.
22 “Inu mudzakhaladi anthu anga+ ndipo ine ndidzakhala Mulungu wanu.”+
23 Taonani! Mphepo yamkuntho yochokera kwa Yehova yawomba. Mkwiyo wake wawomba ngati kamvulumvulu wosakaza.+ Wawomba pamitu ya anthu oipa.+
24 Mkwiyo woyaka moto wa Yehova sudzatha kufikira atachita zofuna za mtima wake ndi kuzikwaniritsa.+ M’masiku otsiriza, anthu inu mudzalingalira zimenezi.+