Yeremiya 52:1-34

52  Zedekiya+ anali ndi zaka 21 pamene anayamba kulamulira,+ ndipo analamulira zaka 11 ku Yerusalemu.+ Mayi ake anali a ku Libina,+ ndipo dzina lawo linali Hamutali,+ mwana wa Yeremiya.  Iye anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova,+ mogwirizana ndi zonse zimene Yehoyakimu+ anachita.  Zimene zinachitika ku Yerusalemu ndi ku Yuda zinakwiyitsa kwambiri Yehova ndipo anawachotsa pamaso pake.+ Kenako Zedekiya anapandukira mfumu ya Babulo.+  Ndiyeno m’chaka cha 9 cha ufumu wa Zedekiya,+ m’mwezi wa 10, pa tsiku la 10 la mweziwo, Nebukadirezara mfumu ya Babulo pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo anabwera ku Yerusalemu+ kudzaukira mzindawo. Atafika anayamba kumanga misasa ndi khoma kuzungulira mzinda wonsewo.+  Choncho mzindawo unazunguliridwa mpaka chaka cha 11 cha Mfumu Zedekiya.+  M’mwezi wachinayi, pa tsiku la 9,+ njala inafika poipa kwambiri mumzindawo, ndipo anthu a m’dzikolo analibiretu chakudya.+  Ndiyeno khoma la mzindawo linabooledwa,+ ndipo amuna onse ankhondo anayamba kuthawa.+ Iwo anatuluka mumzindawo usiku kudzera pachipata chimene chinali pakati pa makoma awiri, pafupi ndi munda wa mfumu,+ ndipo analowera njira yopita ku Araba. Apa n’kuti Akasidi atazungulira mzinda wonsewo.+  Pamenepo gulu lankhondo la Akasidi linayamba kuthamangitsa mfumuyo+ ndipo Zedekiya anamupeza+ m’chipululu cha Yeriko. Zitatero gulu lonse lankhondo la Zedekiya linabalalika n’kumusiya yekha.+  Kenako Akasidiwo anagwira mfumuyo n’kupita nayo ku Ribila,+ kwa mfumu ya Babulo,+ m’dziko la Hamati,+ kuti mfumu ya Babuloyo ikamuweruze.+ 10  Zitatero mfumu ya Babulo inapha ana aamuna a Zedekiya ku Ribila, iye akuona.+ Inaphanso akalonga onse a ku Yuda.+ 11  Mfumu ya Babulo inachititsa khungu Zedekiya+ ndipo kenako inamumanga ndi maunyolo amkuwa n’kupita naye ku Babulo.+ Kumeneko anamuika m’ndende mpaka tsiku la imfa yake. 12  Ndiyeno m’mwezi wachisanu, pa tsiku la 10 la mweziwo, m’chaka cha 19 cha ulamuliro wa Mfumu Nebukadirezara+ ya Babulo, Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu, amene anali kutumikira mfumu ya Babulo, anabwera ku Yerusalemu. 13  Iye anatentha nyumba ya Yehova,+ nyumba ya mfumu ndi nyumba zonse za mu Yerusalemu.+ Anatenthanso nyumba iliyonse ya munthu wotchuka.+ 14  Kenako gulu lonse lankhondo la Akasidi, lomwe linali ndi mkulu wa asilikali olondera mfumu uja, linagwetsa mpanda wonse wa Yerusalemu.+ 15  Anthu onyozeka pakati pa Ayudawo, anthu ena onse amene anatsala mumzindamo,+ anthu amene anathawira ku mbali ya mfumu ya Babulo ndi amisiri onse aluso, Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu, anawatenga kupita nawo ku ukapolo.+ 16  Ena mwa anthu onyozeka a m’dzikolo, Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu uja anawasiya kuti akhale olima minda ya mpesa ndi alimi ogwira ntchito mokakamizidwa.+ 17  Zipilala zamkuwa+ zimene zinali panyumba ya Yehova, zotengera zokhala ndi mawilo+ ndi chosungiramo madzi chamkuwa+ zimene zinali m’nyumba ya Yehova, Akasidi anaziphwanyaphwanya n’kutenga mkuwa wakewo kupita nawo ku Babulo.+ 18  Akasidiwo anatenganso ndowa, mafosholo,+ zozimitsira nyale,+ mbale zolowa,+ makapu ndi ziwiya zonse zamkuwa zimene ansembe anali kugwiritsira ntchito potumikira.+ 19  Mkulu wa asilikali olondera mfumu uja anatenga mabeseni,+ zopalira moto, mbale zolowa,+ ndowa zochotsera phulusa, zoikapo nyale,+ zikho ndi mbale zinanso zolowa zomwe zinali zagolide weniweni,+ komanso zomwe zinali zasiliva weniweni.+ 20  Koma panalibe amene anayeza kulemera kwa mkuwa wa zipilala ziwiri zija,+ chosungiramo madzi chimodzi chija,+ ng’ombe zamkuwa 12+ zija ndi zotengera zokhala ndi mawilo zimene Mfumu Solomo inapangira nyumba ya Yehova.+ Palibe amene anayeza kulemera kwa mkuwa wa ziwiya zonsezi.+ 21  Ponena za zipilalazo, chipilala chilichonse chinali chotalika mikono* 18,+ ndipo chinali kuzunguliridwa ndi chingwe chotalika mikono 12.+ Chipilala chilichonse chinali champhako ndipo kuchindikala kwake kunali kofanana ndi mphipi ya zala zinayi. 22  Mutu wa chipilala chilichonse unali wamkuwa.+ Mutuwo kutalika kwake kunali mikono isanu,+ ndipo maukonde ndi makangaza* amene anazungulira mutuwo,+ onse anali amkuwa. Chipilala chachiwiri chinalinso ndi maukonde ofanana ndi amenewa komanso chinali ndi makangaza.+ 23  Makangaza amene anali m’mbali mwa zipilalazo analipo 96, ndipo makangaza onse amene anali pamaukondewo analipo 100.+ 24  Mkulu wa asilikali olondera mfumu uja anatenganso Seraya+ wansembe wamkulu, Zefaniya+ wansembe wachiwiri, ndi alonda atatu a pakhomo.+ 25  Mumzindawo anatengamo nduna imodzi ya panyumba ya mfumu imene inali kuyang’anira amuna ankhondo. Anatenganso amuna 7 kuchokera pa anthu amene ankatha kuonana ndi mfumu mwa amuna amene anali mumzindamo.+ Komanso anatenga mlembi wa mkulu wa asilikali yemwe anali kusonkhanitsa ankhondo a m’dzikolo, ndi amuna 60 mwa anthu a m’dzikolo amene anali mumzindawo.+ 26  Choncho, Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu anatenga anthuwa n’kupita nawo ku Ribila kwa mfumu ya Babulo.+ 27  Mfumu ya Babulo inapha anthu amenewa+ ku Ribila+ m’dziko la Hamati.+ Choncho Ayuda anachoka kudziko lawo n’kupita ku ukapolo.+ 28  Ziwerengero za anthu amene Nebukadirezara anawatenga kupita nawo ku ukapolo ndi izi: m’chaka cha 7 cha ulamuliro wake, anatenga Ayuda 3,023.+ 29  M’chaka cha 18 cha ulamuliro wa Nebukadirezara,+ anatenga anthu 832 kuchokera ku Yerusalemu. 30  M’chaka cha 23 cha ulamuliro wa Nebukadirezara, Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu anatenga Ayuda 745 kupita nawo ku ukapolo.+ Anthu onse amene anawatenga anali 4,600. 31  Kenako, m’chaka cha 37 cha ukapolo wa Yehoyakini+ mfumu ya Yuda, m’mwezi wa 12, pa tsiku la 25 la mweziwo, chaka chimene Evili-merodaki mfumu ya Babulo anakhala mfumu, iye anakomera mtima Yehoyakini mfumu ya Yuda ndi kumutulutsa m’ndende.+ 32  Kenako anayamba kulankhula naye zinthu zabwino, ndipo anakweza ufumu wake kuposa mafumu ena amene anali naye limodzi ku Babulo.+ 33  Yehoyakini anavula zovala zake za kundende,+ ndipo nthawi zonse anali kudya chakudya+ pamaso pa mfumuyo masiku onse a moyo wake.+ 34  Tsiku lililonse ankapatsidwa chakudya kuchokera kwa mfumu ya Babulo, masiku onse a moyo wake. Anali kumupatsa chakudya chimenechi tsiku ndi tsiku mpaka imfa yake.+

Mawu a M'munsi

Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu.
“Makangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu, mwina chifukwa choti njere zake zimaoneka ngati chimanga.