Yeremiya 6:1-30
6 Bisalani, inu ana a Benjamini, thawani pakati pa Yerusalemu. Ku Tekowa+ imbani lipenga la nyanga ya nkhosa.+ Ku Beti-hakeremu+ kwezani moto wa chizindikiro, chifukwa chiwonongeko chachikulu, tsoka, lasuzumira kuchokera kumpoto.+
2 Ndithudi mwana wamkazi wa Ziyoni wafanana ndi mkazi wachisasati* wooneka bwino.+
3 Abusa ndi magulu awo a ziweto anali kubwera kwa iye. Anamanga mahema awo momuzungulira kuti amuukire.+ Aliyense wa iwo anali kudyetsa ziweto zake pamalo ake.+
4 Anakonzekera kumuthira nkhondo ndipo anati:+ “Nyamukani, tiyeni tipite dzuwa lili paliwombo!”+
“Tsoka ife chifukwa nthawi yatithera ndipo zithunzithunzi zikupitiriza kutalika!”
5 “Nyamukani, ndipo tiyeni tipite usiku kuti tikawononge nsanja zake zokhalamo anthu.”+
6 Pakuti Yehova wa makamu wanena kuti: “Dulani mitengo+ kuti tipangire Yerusalemu chiunda chomenyerapo nkhondo.*+ Yerusalemu ndi mzinda woyenera kuimbidwa mlandu.+ Mkati mwake muli kuponderezana kokhakokha.+
7 Monga mmene chitsime chimasungira madzi ake ali ozizira, Yerusalemu wasunga zoipa zake ngati zinthu zabwino. Mkati mwake mumamveka zachiwawa ndi kufunkha.+ Nthawi zonse ndimaona matenda ndi miliri mumzindawo.
8 Iwe Yerusalemu, mvera chilango+ kuti ndisatembenuke ndi kukufulatira chifukwa chonyansidwa nawe,+ kuti ndisakusandutse bwinja, dziko lopanda munthu aliyense wokhalamo.”+
9 Yehova wa makamu wanena kuti: “Mosalephera adani adzakunkha otsalira a Isiraeli ngati mmene amakunkhira mphesa.+ Kweza dzanja lako ngati munthu amene akuthyola mphesa panthambi za mtengo wa mpesa.”
10 “Kodi ndilankhule ndi ndani ndipo ndichenjeze ndani kuti amve? Taonani! Makutu awo sanawachite mdulidwe, moti sangamve.+ Taonani! Mawu a Yehova akhala onyozeka kwa iwo,+ ndipo sakukondwera nawo.+
11 Ndadzazidwa ndi mkwiyo wa Yehova. Ndatopa ndi kukhala chete.”+
“Tsanulira mkwiyowo pa mwana amene ali mumsewu+ ndipo nthawi yomweyo uutsanulirenso pa kagulu ka anyamata okondana. Mwamuna pamodzi ndi mkazi wake, munthu wachikulire pamodzi ndi munthu wokalamba, onsewo adzagwidwa.+
12 Nyumba zawo, minda yawo ndi akazi awo, zonse pamodzi zidzaperekedwa kwa anthu ena.+ Pakuti ine ndidzatambasula dzanja langa ndi kuwononga anthu okhala m’dzikoli,” watero Yehova.+
13 “Pakuti aliyense wa iwo, kuyambira wamng’ono mpaka wamkulu akupeza phindu lachinyengo.+ Kuyambira mneneri mpaka wansembe, aliyense wa iwo akuchita zachinyengo.+
14 Iwo akuyesa kuchiritsa mwachinyengo+ kuwonongeka kwa anthu anga ponena kuti, ‘Kuli mtendere! Kuli mtendere!’ pamene kulibe mtendere.+
15 Kodi iwo anachita manyazi chifukwa chochita zinthu zonyansazi?+ Iwo sanachite manyazi ngakhale pang’ono, komanso sadziwa n’komwe kuchita manyazi.+ Choncho iwo adzagwa pamodzi ndi anthu amene akugwa.+ Pamene ndidzakhala ndikuwaimba mlandu adzapunthwa,” watero Yehova.
16 Yehova wauza anthuwo kuti: “Imani chilili panjira anthu inu, kuti muone ndi kufunsa za njira zakale, kuti mudziwe kumene kuli njira yabwino.+ Mukaipeza muyende mmenemo+ kuti mupeze mpumulo wa miyoyo yanu.”+ Koma iwo anapitiriza kunena kuti: “Ife sitiyendamo.”+
17 “Koma anthu inu ndinakuutsirani alonda+ ndipo ndinati, ‘Mverani kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosa!’”+ Koma iwo anapitiriza kunena kuti: “Ife sitidzamvera.”+
18 “Choncho tamverani, inu mitundu ya anthu, kuti mudziwe anthu inu, zimene zidzawachitikira.
19 Tamverani, inu okhala padziko lapansi! Ine ndikubweretsa tsoka pa anthu awa+ chifukwa cha maganizo awo,+ pakuti sanamvere mawu anga ndipo anapitirizabe kukana chilamulo changa.”+
20 “N’chifukwa chiyani mukundibweretsera lubani* wochokera ku Sheba+ ndi mabango onunkhira ochokera kudziko lakutali? Zimenezi zili ndi ntchito yanji kwa ine? Nsembe zanu zopsereza zathunthu sizikundisangalatsa,+ ndipo nsembe zina zonse zimene mukupereka sizikundikondweretsa.”+
21 Choncho Yehova wanena kuti: “Tsopano ndikuikira anthu awa zinthu zopunthwitsa,+ ndipo onse pamodzi, abambo ndi ana, adzapunthwa pa zinthu zimenezi, munthu aliyense limodzi ndi mnzake adzatheratu.”+
22 Yehova wanena kuti: “Taonani! Anthu akubwera kuchokera kudziko la kumpoto. Pali mtundu wamphamvu umene udzadzutsidwa kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+
23 Iwo adzagwira uta ndi nthungo.*+ Umenewu ndi mtundu wankhanza ndipo sudzachita chisoni. Mawu awo adzamveka ngati mkokomo wa nyanja+ ndipo adzabwera pamahatchi.+ Mtunduwo wafola pokonzekera kumenya nawe nkhondo ngati mmene mwamuna wankhondo amachitira, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni.”+
24 Ife tamva uthenga wa zimenezi. Manja athu angoti lendee!+ Tagwidwa ndi nkhawa ndipo tikumva ululu ngati wa mkazi amene akubereka.+
25 Musatuluke kupita kunja ndipo musayende m’njira pakuti kumeneko kuli lupanga la mdani. Zochititsa mantha zili paliponse.+
26 Iwe mwana wamkazi wa anthu anga, vala chiguduli*+ ndi kuvimvinizika m’phulusa.+ Lira ngati kuti ukulira maliro a mwana wamwamuna mmodzi yekhayo. Lira mowawidwa mtima+ chifukwa wofunkha adzatiukira modzidzimutsa.+
27 “Ndakusandutsa woyesa zitsulo pakati pa anthu anga. Ndakusandutsa wofufuza mosamala ndipo udzaonetsetsa ndi kufufuza njira zawo.+
28 Onse ndi anthu ouma khosi kwambiri,+ oyenda uku ndi uku ngati anthu amiseche.+ Iwo ali ngati mkuwa ndi chitsulo. Onsewo ndi anthu owononga.+
29 Zipangizo zopemerera moto+ zatenthedwa ndi moto ndipo pamoto wawo pakutuluka mtovu.+ Munthu wakhala akuyenga chitsulo mobwerezabwereza koma osaphula kanthu, ndipo zoipa sizinachotsedwemo.+
30 Anthu adzawatcha, ‘siliva wokanidwa,’+ pakuti Yehova wawakana.”+
Mawu a M'munsi
^ Munthu “wachisasati” ndi munthu wopusa chifukwa chakuti anamulera momulekerera ndipo sanaphunzire ntchito kapena zinthu zina zomuthandiza pamoyo wake.
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Tikati nthungo tikutanthauza mkondo waung’ono, wopepukirako.
^ Ena amati “saka.”