Yeremiya 28:1-17

28  Ndiyeno m’chaka chimenecho, chaka chachinayi, m’mwezi wachisanu, kuchiyambi kwa ufumu wa Zedekiya+ mfumu ya Yuda, Hananiya+ mwana wa Azuri, mneneri wa ku Gibeoni,+ anauza Yeremiya m’nyumba ya Yehova pamaso pa ansembe ndi anthu onse kuti:  “Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Ndithyola goli la mfumu ya Babulo.+  Pa zaka ziwiri zokha ndibwezeretsa pamalo ano ziwiya zonse za m’nyumba ya Yehova zimene Nebukadinezara mfumu ya Babulo+ anatenga pamalo ano ndi kupita nazo ku Babulo.’”  “‘Ndipo Yekoniya+ mwana wa Yehoyakimu,+ mfumu ya Yuda, ndiponso anthu onse a mu Yuda amene anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo+ ndiwabwezeretsa kuno, pakuti ndithyola goli+ la mfumu ya Babulo,’ watero Yehova.”  Pamenepo mneneri Yeremiya anayankha mneneri Hananiya pamaso pa ansembe ndi anthu onse amene anali chilili m’nyumba ya Yehova,+  inde, Yeremiya anayankha kuti: “Zikhale momwemo!*+ Yehova achitedi zimenezo! Yehova akwaniritse zonse zimene walosera m’mawu ako. Achite zimenezo mwa kubwezeretsa pamalo ano ziwiya za m’nyumba ya Yehova ndi anthu onse amene anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo!+  Komabe, tamvera mawu amene ndikufuna kukuuza pamaso pa anthu onse.+  Aneneri akalekale amene analiko ineyo ndisanakhalepo komanso iweyo usanakhalepo+ anali kuloseranso za nkhondo, masoka ndi miliri yoti igwere mayiko ambiri ndi maufumu amphamvu.+  Koma mneneri amene walosera za mtendere+ amadziwika kuti ndi munthu amene Yehova wamutumadi ulosi wakewo ukakwaniritsidwa.”+ 10  Hananiya atamva zimenezo anatenga goli limene linali m’khosi mwa mneneri Yeremiya ndipo analithyola.+ 11  Kenako Hananiya+ anauza anthu onse amene anali pamenepo kuti: “Yehova wanena kuti,+ ‘Pa zaka ziwiri zokha, ndithyola goli la Nebukadinezara mfumu ya Babulo limene waveka mitundu yonse ya anthu monga mmene ndathyolera goli ili.’”+ Zitatero, Yeremiya anachokapo.+ 12  Mneneri Hananiya atathyola goli limene linali m’khosi mwa mneneri Yeremiya,+ Yehova anauza Yeremiya kuti: 13  “Pita ukauze Hananiya kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Iwe wathyola magoli+ amtengo, ndipo tsopano m’malomwake padzakhala magoli achitsulo.”+ 14  Pakuti Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti: “Ndidzaika magoli achitsulo pamakosi a mitundu ya anthu yonseyi kuti atumikire Nebukadinezara mfumu ya Babulo,+ ndipo ndikunenetsa kuti adzamutumikiradi.+ Nebukadinezara ndidzamupatsanso ngakhale nyama zakutchire.”’”+ 15  Pamenepo mneneri Yeremiya anauza mneneri Hananiya+ kuti: “Tamvera iwe Hananiya! Yehova sanakutume, koma iwe wachititsa anthuwa kukhulupirira zinthu zonama.+ 16  Chotero Yehova wanena kuti, ‘Ndikukuchotsera moyo wako. Chaka chomwe chino iweyo ufa,+ chifukwa zimene wanenazo ndi kupandukira Yehova kwenikweni.’”+ 17  Choncho mneneri Hananiya anamwalira chaka chomwecho, m’mwezi wa 7.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “Ame!” m’Chiheberi.